Genda galu kuti udziwe mwini wake: kuchotsedwa kwa anthu ku DPP kwakwiyitsa MCP

Advertisement
Chazama, Jeffrey and Dausi at the NGTC meeting where Chazama represented DPP leader Pe6ter Mutharika

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chati ndichokhumudwa ndi zomwe chapanga chipani cha Democratic Progressive (DPP) pochotsa ma membala ake ena mu chipanicho kuphatikiza a Kondwani Nankhumwa; koma anthu ena akuti ukafuna kudziwa mbuyake wa galu, umatola duka ndikum’gweba nalo pomwe ena akuti agalu otumidwa aja adya zothira tameki ndipo mwini agaluwo wakwiya.

Nkhaniyi yayamba pomwe Loweruka usiku pa 20 January, 2024, chipani cha DPP chatulutsa kalata yolengeza kuti chachotsa mchipani mamembala ake angapo omwe ndikuphatikiza a Nankhumwa, Grezelder Jeffrey, Mark Botomani, Nicholas Dausi, Cecilia Chazama kungotchulapo ochepa chabe.

Potsatira zomwe chapanga chipani chotsutsa bomachi, chipani cha MCP nacho chatulutsa kalata Lamulungu pa 21 January, 2024 momwe yanena m’maso muli mbee kuti ndichokhumudwa kuti chipani cha DPP chatulutsa makosanawa zomwe akuti ndikutsutsana ndi mfundo za demokalase zomwe zimalimbikisa kugonjerani, komaso kulolerana.

Mu kalata yomwe wasainira ndi mneneri wa chipani cha MCP a Ezekiel Ching’oma, chapanichi chati potengera nkhani ya demokalase, chipani chawo chikuona kuti kunali kosafunikira kuti chipani cha DPP chifike powonetsa nsana wa njira makosanawa amenewa.

“Chipani cha Malawi Congress chakhudzidwa kwambiri ndi zomwe zachitika posachedwapa za kuthamangitsidwa kwa mamembala a chipani cha Democratic Progressive (DPP). Zochita za chipani chotsutsazi n’zosemphana ndi mfundo za demokalase zomwe zimalimbikitsa kufunikira kokambirana, kutenga nawo mbali, ndi kulolerana popanga  ziganizo, komanso ufulu wa ndale ndi ufulu wosonkhana womwe A laMalawi onse amatsimikiziridwa ndi malamulo oyendetsera dziko lathu.

“Choncho ndi zokhumudwitsa kuona chipani chotsutsa chikuchita zinthu zopanda demokalase zomwe DPP yachita, zomwe zikusokoneza demokalase ya dziko lathu komanso mfundo zomwe chipanicho chidakhazikitsidwa. Chipani cha ndale nthawi zonse chiyenera kukhala chomasuka ku malingaliro osagwirizana ndi mamembala ake ndikupereka njira zotsutsirana, ndemanga, ndi kuyanjanitsa. Koma pochotsa mwachidule mamembala ake pogwiritsa ntchito njira yosokonekera, DPP yakhazikitsa chitsanzo choipa chomwe chikuwopseza demokalase ya dziko lathu,” yatelo mbali ina ya kalata ya MCP.

Chipani cha Malawi Congress chati chikupempha chipani cha DPP ndi utsogoleri wake kuti azitsatira mfundo za demokalase ndipo chati chikupempha chipani cha DPP kuti chiwunikenso zochita zake ndikugwirizana ndi zipani zina m’Malawi muno pakukhala ndi mtima wokonda anthu onse komanso kuchita zinthu mwapoyera.

Pakadali pano anthu makamaka m’masamba anchezo, alandira mosiyanasiyana zomwe chipani cha MCP chayankhulazi ndipo ena akuti ichi ndichitsimikizo choti chipanichi cholamulachi chimamva kukoma pomwe mpungwepungwe umakanika kutha nchipani cha DPP.

“Zazii!!! Ndikuona kuti MCP yakhudzidwa kwambiri ndiye kuti amene achotsedwawo ndi omwe amaba info kumapereka ku MCP nanga mmalo moti mukhale busy ndikulongosola dziko lomwe likukuvutanili muli busy kulongosola za chipani cha eni,” watelo munthu wina yemwe anaikira ndemanga za nkhaniyi pa tsamba lathu la fesibuku.

Anthu enaso akumbutsa chipani cha MCP kuti nacho m’mbuyomu chinachotsa anthu ena omwe ankazunguza kuphatikizapo a Richard Msowoya, Gustavo Kaliwo ndi a Jessie Kabwila.

Advertisement