Boma latsindika ku mtundu wa a Malawi kuti limanga mabwalo amasewero a matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets mu mzinda wa Blantyre.
Nduna yoona za achinyamata ndi masewero mdziko muno a Uchizi Mkandawire ndi omwe atsindika za nkhaniyi.
Ntchito yomanga mabwalo amasewerawa alengezedwa koyamba mchaka cha 2020 koma idayamba yayima kaye. Kotero ndunayi yatsindika ku mtundu wa a Malawi kuti ntchitoyi iyambiranso mpaka kufika poti yatha moyenera.
Boma lanena izi kutsatira lonjezo lomwe mboyomu lidalonjeza kuti limanga mabwalo amasewerowa.
One comment on “Boma latsindika kuti limanga mabwalo amasewera a Bullets ndi Wanderers”
Comments are closed.

Koma ndi ganizo labwino . Zangolakwika awunjika mu Blantyre Mokha. Nanga ku Mzuzu Lilongwe?