Mfumu Chawola ya dera la Kangoi yomwe ili pansi pa Mfumu ya yikulu Timbiri M’boma la Nkhata Bay yati iyo limodzi ndi anthu awo ndiwokondwa kuti tsopano ntchito za umoyo pa chipatala chaching’ono cha Kangoi ziyamba kuyenda bwino.
Mfumuyi yanena izi pomwe Bambo Lloyd Ndhlozi omwe akufuna kuzapikisana pa mpando wa ukhansala ku wadi ya Mwambazi amanga nyumba ya mlangizi wa zaumoyo pa Chipatalachi, chomwe chakhala zaka zambiri popanda mlangizi waza umoyo.
“Ndine wokondwa kwambiri kuti tsopano tikhala ndi mulangizi waza umoyo pa kiliniki yathu, yomwe yakhala nthawi yayitali popanda mulangizi kamba ka vuto lakusoweka kwanyumba yokhalamo, koma pano ndi nyumba yomwe a shado khansala bambo Lloyd Ndhlozi atimangira vuto lakusowa kwa mulangizi waza umoyo kudera langa ili likhala mbiri yakale,” adatero a Mfumu Chiwola.
Bambo James Chioni Chimphoyo omwe ndi wapampando wa komiti ya Chipatalachi awuza Malawi24 kuti kumangidwa kwa nyumbayi pa chipatalachi kwathetsa mavuto omwe mlangizi amakumana nawo maka kumayenda mtunda wawutali kuchokera ku Chikwina ndipo nthawi zina amafika mochedwa kamba kamayendedwe.
“Tithokoze ofesi ya za umoyo ya Nkhata Bay yomwe ya titumizira mulangizi waza umoyo. Amai a dera lathu amayenda mtunda wautali kukafuna thandizo koma pano anthu azithandizikira pafupi” Anatero a Chimphoyo.
M’mau awo bamboo, Lloyd Ndhlozi ati anthu okhala mdera la Mwambazi wadi akukumana ndi mavuto ambiri, koma ati anaganiza kuti akonze kaye vuto lakusowa kwa mlangizi wa zaumoyo kudera la Kangoi pomanga nyumba yokhalamo mlangiziyo.
“Angakhale kuti derali kuli mavuto osiyana siyana koma ndinaona kuti ndiyambe kaye ndathetsa vuto la kusoweka kwa mlangizi wa za umoyo, pomanga nyumba pa Chipatala Chaching’ono cha Kangoi. Ndine wokondwa kuti ntchitoyi yayenda bwino ndipo pano tikuyika malata, posachedwapa nyumbayi mlangiziyi alowamo,” anatero a Ndhlozi.
Iwo alimbikisanso anthu akuderali kuti apitilize kutengapo gawo pa nkhani za chitukuko zomwe zikubwera kuderali.
Ndhlozi ati kusiyana kwa zipani zomwe akutsatira kuderali kusawagawanitse pankhani yotengapo mbali pa chitukuko.
Gogo Timbiri nawo ayamikira zintchito za a Ndhlozi ponena kuti masomphenya abwino omwe ali nawowa apitilize, ndipo iwo alangiza onse akufuna kuzapikisana nawo pa zisankho za 2025 pa ma undindo wosiyana siyana kuti akonzekere kukhazikitsa fundo za chitukuko zomwe atha kuzakwanitsa.
Bambo Lloyd Ndhlozi ndi Mlembi wa mkulu wa Chipani cha Freedom ku chigawo cha kumpoto, chipani chomwe chikutsogozedwa ndi wachiwiri wa mtsogoleri wakale wadziko lino a Khumbo Kachale.
Iwo anatengelaponso mwayi kunena kuti chipanichi chachilimika kuti anthu ake azawatumikire mtundu wa Malawi.