Tsopano Mavuto Phiri ndi mfulu popeza bwalo la milandu ku Karonga lathetsa mlandu womwe wakhala akuganizilidwa kuti adapha mchimwene wake mchaka cha 2018 pa mkangano omwe udabuka pakati pa abambo ake ndi mchimwene wake amene amaganizira kuti abambo akewo adali kuchita ubwenzi wanseli ndi mkazi wake.
Nkhani yonse ikuti m’mwezi wa September mchaka cha 2018, mkangano udabuka pakati pa abambo ake a Mvuto ndi mchimwene wake kaamba koti mchimwene wakeyo adali kuganizira kuti abambo akewo adali kuchita ubwezi wanseli ndi mkazi wake.
Izi zinakwiyitsa kwambili mnyamatayu mpakana adayamba kukangana ndi bambo akewo. Apa mkuti bambowo adali atanyamula mpeni komanso botolo la bibida m’manja.
Powona kuti mkangano wakula pakati pa abambo ake ndi mchimwene wakeyo, Mavuto adalowelera kuti akateteze bambo akewo poti mnyamatayu adali atazaziratu.
Apa mchimwene wakeyo adateleleka ndikugwa pansi, koma mwangozi, adagwera pa mpeni ndi botolo lamowa lija.
Mavuto powona kuti mchimwene wakeyo wavulala kwambili, adathamangira naye kuchipatala komwe adauzidwa kuti mchimwene wakeyo adali atamwalira kale.
Apolisi aku Chilumba atamva za nkhaniyi sadachedwe koma kukamunjata Mavuto pomuganizila kuti adadzetsa imfa kwa mchimwene wakeyo.
Iye anamangidwa, adapempha belo yomwe adamupatsa uku akudikilira mlandu wake. Iye anakapemphanso thandizo ku Malawi Legal Aid Bureau ndipo lidamuvomera kumuyimira pa mlandu wake onse.
Apa amene oyimira mlandu waboma adauza bwalo lamilandu kuti zina mwa mboni zomwe zikuyenera kudzakhalapo pa mlandu ndi abale ake a Mavuto yemwe amaganiziradwa kuti adapha mchimwene wakeyo.
Patapita nthawi powona kuti abale amavuto samabwera kudzaperekera umboni, ambali ya boma adafotokozera Justice Justuce Kishindo kuti Mavuto angomumasula chifukwa mboni sizikubwera.
Apa mpamene bwalo la milandu la High Court, kudzera mwa oweluza milandu pa bwaloli adamva pempholi ndikumumasula Mavuto ndikuthetsa mlanduwu poona kuti padalibe mboni zomwe zidali kubwera