La fote lakwana! Bambo wina walilime lakuthwa yemwe ndi wa zaka 39 ali m’manja mwa apolisi ku Lilongwe pomuganizira kuti wakhala akufusira amayi pa tsamba la nchezo la fesibuku ndikuwalonjeza kuti awakwatira koma akakumana nawo amawabera katundu kapena ndalama ndikuthawa.
Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu omwe azindikira bambo ochenjera pakamwayu ngati a Ramsey Samuel omwe akuti amangidwa Lachinayi pomwe akhala akupalamula milandu ya mtunduwu kwa nthawi yaitali.
A Chigalu ati chatsitsa dzaye nchakuti monga mwa chizolowezi chawo, mu September chaka chatha a Samuel anafunsira mayi wina wochokera ku Kasungu yemwe akuti anamulonjeza kuti amukwatira ndipo naye mayiyo mphuno salota anagonekera khosi ndipo anavomera kugwa nchikondi ndi kathyaliyu.
Mkati mwa ulendo wa chikondi, awiriwa anagwirizana kuti mkaziyu achoke ku Kasungu ndipo atsatire a Samuel ku Lilongwe, koma ati a njondayi inakanitsitsa mwa ntu wagalu kutumizira ndalama ya thalasipoti nthiti yakeyo ndipo m’malo mwake iwo analonjeza kuti mkaziyu akongole ndalama ndipo adzamubwezera awiriwa akakumana.
Mayiwa atafika ku Lilongwe anakumanadi ndi bamboyu ndipo onse anagona limodzi pamalo ogona alendo ku Mitundu.
Mam’mamawa pomwe mayiyu amasamba, a Samuel anaba ma foni awiri a ndalama yokwana K180,000 kenaka ndikuliyatsa liwilo la mtondo wadooka ndipo momwe mayiwa amatuluka ku bafa anangoti kukamwa yasa.
Malingana ndi apolisi, amayi enaso okwana asanu ndi modzi (6), anadandaulaposo kuti a Samuel anawapanga chipongwe chonga ichi zomwe zinapangitsa kuti apolisi akhazikitse kafukufuku osaka nkulu odyera pakamwayu yemwe pano wanjatwa tsopano ndipo akudikira kukaonekera ku khothi posachedwapa.
A Ramsey Samuel omwe amachokera m’mudzi wa Chidzulumbi ku Lilongwe ovemera kupalamura mlanduwu ndipo awulura kuti anaberaposo amayi ena atatu mwa njira imeneyi.