Sukulu ku Zambia zikhalabe zotseka kamba ka Cholera

Advertisement

Dziko la Zambia, lomwe ndi neba wa Malawi, lati sukulu ku Zambia zikhalabe zotseka mpaka pa 29 January, 2024  kamba ka muliri wa cholera womwe wabuka m’dzikoli.

Chikalata chomwe unduna wa za maphunziro mogwirizana ndi unduna wa za umoyo watulutsa chati sukulu zonse zaboma komaso zomwe si za boma zaimitsidwa kaye ngati njira imodzi yochepetsa kufala kwa muliriwu.

Teremu yoyamba mu chaka chino yomwe imayenera kuyamba pa 8 January tsopano idzayamba pa 29 January.

Izi zili chomwechi kamba ka kukwera kwa chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi kolera. Kuchokera mu October chaka chatha kufika dzulo pa 3 January, 2024 athu okwana 128 amwalira ndi Cholera ku Zambia koma pa 2 January pokha anthu 16 anamwalira. Anthu omwe apezeka ndi Cholera kuyambira mu October ndi oposa 3,757.

Pakadali pano, unduna wa za umoyo mothandizana ndi bungwe la UNICEF komaso World Health Organisation ali kalikiliki kudziwitsa anthu njira zomwe angatsate kuti apewe muliriwu monga kusamba m’manja komaso kugwiritsa ntchito madzi a ukhondo.

Advertisement