Reserve Bank of Malawi (RBM), yomwe ndi banki yayikulu m’dziko muno, yachenjeza kuti ithana ndi aliyense amene apezeke akukana ndalama ponena kuti inatha mphamvu ndipo potsindika za nkhaniyi a RBM ati ngakhale ma 1 tambala ndi ovomerezeka kugulira chinthu.
Malingana ndi mneneri wa bankiyi, Dr Mark Lungu wati a Malawi akuyenera azipanga lipoti munthu amene akukana ndalama ponena kuti idatha mphamvu.
A Lungu anapitiliza kufotokoza kuti khalidwe lokana ndalama zina ponena kuti zidatha mphamvu ndilotsutsana ndi ndondomeko zokhudza malonda zomwe ati zimalora munthu ofuna kugula malonda kugwilitsa ntchito ndalama iliyonse yadziko lino.
Potsindika za nkhaniyi, mneneriyu anafotokozanso kuti angakhale ma 1 tambala ndi otheka kugulira zinthu ndipo anthu asadzanamizidwe kuti idasiya kugwira ntchito.
Izi zadza kutsatira amalonda ochuluka mdziko muno amakana ndalama zina monga K10 yomwe ili ya chitsulo komanso K20 yomwe ili ya pepala ponena kuti zidatha mphamvu chifukwa cha kugwa ndalama ya Kwacha.