Bungwe la Malawi Kickboxing Association lati likufuna ndalama zocholuka zoyendetsera masewero

Advertisement

Bungwe la Malawi Kickboxing Association lati likufuna ndalama zocholuka zoyendetsera masewero otibulana a kickboxing ndipo lapempha Boma kudzera ku Malawi Sports Council kuti liwathandidze.

Mlembi wamkulu ku Bungwe la Malawi Kickboxing Association a Bright Limani ndiwomwe ayankhula izi Lolemba ku China Complex ku Zomba komwe kudali masewero a Inter Club Kickboxing Championship ofuna kusankha akaswiri amasewerowa.

A Limani adati ndalama zomwe amalandira ndizochepa choncho pakufunika ndalama zambiri pofuna kupititsa patsogolo masewero a kickboxing muno Malawi.

Iwo adati ndiwokhutitsidwa ndi momwe masewerowo adayendera ndipo adathokodza ma club ochokera Zomba, Blantyre, Mangochi komanso Thyolo chifukwa chobwera kudzatenga nawo mbali pampikisanowo.

“Tikufuna chaka chamawa mwezi wa June tidzakonze mpikisano waukulu omwe tidzayitanitse ma club akunja monga Namibia ndi Zimbabwe ndipo lero titsankha anyamata omwe adzimire dziko la Malawi.” Adatero Lamani.

Mu mau ake, yemwe adapambana  pa mpikisanowo Hopeson Nots yemwe ndiwochokera ku Club ya Blantyre Youth Center ndipo adagonjetsa Lucky Rabison wochokera ku Bangwe Wushu Club pama pointi adati chinsinsi chake chidagona polimbikira nthawi yomwe amakonzekera masewerowo.

Nots adati ngakhale wapambana pampikisanowo sadali okondwa chifukwa ndalama zomwe adalandira sidzidali zambiri ayi ndipo adapempha ma company komanso anthu akufuna kwabwino kuti athandidze ndi ndalama kumasewero a kickboxing.

Advertisement