Pulofeti wanjatidwa kamba kogwililira mkazi wamwini

Advertisement

Pulofeti wina kwa Jenda ali m’manja mwa apolisi kamba kogwililira mkazi wamwini yemwe anapita ku tchalitchi cha mneneriyu kuti akamupempherere pa vuto lakusowa mphatso ya mwana m’banja.

Mayiyu yemwe wakhala miyezi itatu m’banja koma osatenga pakati, anaganiza zopita ku tchalitchi cha mneneriyu kuti akamupempherere kamba kavutoli.

Chodabwitsa mchakuti mayiyu atafika ku tchalitchi cha mneneriyu yemwe dzina lake ndi Rodgers Mkandawire, anamutengera mayiyu kukachipinda kena kuti akamupempherere.

Ali ku kuchipindako, mneneriyu adamuuza mayiyu kuti wina adamulodza.  Kenako mneneriyu adatenga phulusa ndikumupaka mayiyu kumalo obisika. Apa mneneriyu ndipo adapezerapo mwayi ochita naye zadama.

Mayiyu atayipidwa ndi zomwe anachita mkuluyu, iye anakauza amuna ake za nkhaniyi omwe anakayitengera ku polisi ya kwa Jenda kenako apolisi sanazengereze koma kukamuthira dzingwe mneneriyo ndikumutsegulira mlandu ogwililira.

A Mkandawire amachokera m’mudzi mwa a Chabwachabwa mdera ya mfumu yayikulu Mthwalo ku Mzimba.

Advertisement