Bambo amulamula kukakhala ku ndende kwa zaka 21 kamba kogwililira mwana


Mkulu wina wa zaka 35 zakubadwa ku Lilongwe walamulidwa kukakhala ku ndende ndikukagwila ntchito ya kalavula gaga kwa zaka 21 kamba kopezeka olakwa pa mlandu wogwililira mwana wa zaka khumi.

Malingana ndi mneneri wa apolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu, nkhani yonse ikuti mkuluyu yemwe dzina lake ndi Zakaliya Potifala adapempha mwanayo kuti akawatungire madzi ku chitsime.

Apa mwanayo atapeza kuti kuchitsimeko kudalibe madzi, mkuluyo adamduduluzira mwanayo m’nyumba ndikumuchita zamalawulozo.

Pamapeto pake, mkuluyu adatenga K300 ndikumpatsa mwanayo ngati chitseka pakamwa koma izi sizidakondweretse mwanayo mpaka adapita kukwawuza amayi ake zamalodzazo.

Koma nkhaniyi itafika pa bwalo la milandu la Principal Magistrate ku Lilongwe, mkuluyo anawuvomera mlanduwu koma iye adafotokoza kuti ndi Satana chabe anamutuma ndipo adapempha oweluza kuti amumvere chisoni koma izi sizinaphule kanthu.

Yemwe ndi oyimira mlandu waboma a Florence Mlanje anati mkuluyu akuyenera kulandira chilango chokhwima potengera msinkhu wa mwanayu komanso kukula kwa mlanduwu ndikuti enanso atengerepo phunziro.

Apa woweluza anagwilizana nazo ndipo analamula a Potifala kuti akakhale ku ndende kwa zaka 21.

Mkuluyu amachokera m’dera la mfumu yayikulu Kwataine ku Ntcheu m’mudzi mwa Mingola.