Papa wati mpingo wakatolika uzidalitsa anthu a paubwenzi wa amuna kapena akazi okhaokha

Advertisement
Pope Francis has approved the blessing of same-sex marriage in Catholic Church

Papa Francis waloleza mpingo wa Katolika pa dziko lonse, kuphatikizapo kuno ku Malawi, kuti uzidalitsa anthu a pa maubwenzi a amuna kapena akazi okhaokha.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe yatulutsa ofesi yoona za malamulo oyendetsera mpingo ku Vatican.

Papa yemwe ndi mkulu wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse wati ansembe asakanize kapena kulepheretsa anthu kukhala chifupi ndi tchalichi pa nthawi iliyonse yomwe anthu angapemphe mdalitso, ngakhale kuti anthuwa ali pa maubwenzi a amuna kapena akazi okhaokha.

Koma Papa wati kudalitsa anthu a pa maubwenzi a amuna kapena akazi okhaokha sikukusonyeza kuti mpingowu ukuvomereza maukwati otere koma kukungosonyeza kuti Mulungu amalandila anthu onse.

Tchalichi cha katolika chimaphunzitsa anthu ake kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndi tchimo koma kukonda mamuna nzako kapena mkazi nzako si tchimo.

Pakali pano, wansembe James Martin yemwe amalalikila kwa anthu omwe amagonana amuna kapena akazi okhaokha wati zomwe wachita Papa ndi njira imodzi yopititsa patsogolo tchalichi.

Ku Malawi, mpingo wa Katolika ndi imodzi mwa mipingo yomwe simalola kuti amuna kapena akazi azikwatirana okhaokha.

Advertisement