Adindo awapempha kuti achite machawi kuthetsa nkangano omwe wafika posauzana m’mudzi mwa mfumu Limera m’boma la Machinga komwe anthu sakumwerana madzi, ndipo akumamenyana pali ponse pomwe angakumanepo kamba ka malo olima mpunga omwe akulimbirana.
Tsamba lino lapeza kuti anthu a m’mudzi mwa mfumu Limera akulimbirana malo ena olima mpunga omwe ali kufupi ndi nyanja ya Chiuta ndipo zikuveka kuti nkanganowu unayamba pafupifupi zaka zitatu zapitazo ndipo magulu awiriwa akukanika kumvana chimodzi za malowa.
Munthu wina yemwe sanafune kutchulidwa dzina mu nkhani ino, watiuza kuti muzaka za m’ma 1940, ku mdera la mfumu Limera kudabwera anthu odzapempha malo okhala ndipo adapatsidwa m’mbali mwa dambo la nyanja ya Chiuta, malo omwe padali mtunda oti atha kumanga komaso nkumalima chimanga ndi mbewu zina.
Munthuyu wati nthawi itadutsa cha m’ma 2010, nyanja ya Chiuta idayamba kuphwera ndipo anthu amudzi wonse kuphatikizapo aja adapempha malo aja adayamba kumagawiridwa dambo la nyanja lija kuti azilima mpunga ndipo mfumu Limera inkatolera mpunga kwa alimi onse ngati zopereka kwa mfumuyo kuti akugwititsa ntchito malo awo.
Mu zaka za pakati pa 2014 ndi 2016, zikuveka padabuka mkangano wa malo pakati pa mfumuyi ndi mfumu Mphonde yomwe mudzi wake uli tsidya lina la nyanja ya Chiuta ndipo mfumu Limera kuphatikozapo anthu omwe adadzapempha malowa aja, adamenyera limodzi nkhondoyo mpaka atapita kukhoti chigamulo chidawakomera.
Malawi24 yauzidwaso kuti mchaka cha 2020 athu omwe anapempha malo mmudzimu adayamba kudandaula kamba kazopereka zomwe amapereka kwa mfumu zija ndipo pa zokambirana adagwirizana kut onse asiye kupeleka mpungawo kwa mfumu yawoyo ndipo zinathekadi mosavuta
Kenaka mu 2021, anthu odzapempha malo aja adawukira mfumu Limera ponena kuti kamba koti iwo akhalitsa mmudzimu, nawoso ndi mzika ndipo akufuna kuti nawo akhale ndi gawo lawo la malo zomwe sizidakomere mfumu Limera yanthawiyo ndipo kukangana kudayamba.
Mkanganowu udapitirira kufikira pomwe mfumu Limera ya nthawiyo idamwalira ndipo italowa mfumu ina, mkanganowu udapitirira ndipo zidafika poti anthu opempha malowa adayamba kumabweza azawowo ponena kuti sakuyenera kulima ku madamboko chifukwa amakhala kuntunda zomwe zidachititsa kuti anthuwa azimenyana mpaka ena kuvulazidwa.
Nkanganowu unafika posauzana sabata yatha pomwe anthu a mbali ya yodzapempha malowa anabweza anthu a mbali ya mfumu Limera kupita ku damboko komwe amafuna akalime mpunga.
Anthuwa anafika potulutsirana zikwanje ndi kukhapana moti tikukamba pano munthu m’modzi akulandirabe thandizo la mankhwala pa chipatala cha bomali pomwe ena osachepera khumi, analandira thandizo ngati odwala oyendera.
Munthuyu wapempha akuluakulu aboma kuti achitepo kanthu nsanga zinthu zisanafike mlingo wina woyipa ponena kuti anthu a mbali yopempha malowa palipose pomwe angakakumane ndi anthu a mbali ya mfumu Limera, akumamenyana zomwe akuti zikupeleka chiwopsezo kuti wina atha kutaya moyo.
“Zinthu sizili bwino. Panopatu nkanganowu wafika poti mbali ziwirizi zikumangokhalira kumenyana paliponse pomwe zingakumanepo. Ife ngati anthu akudelari tinakakonda kuti boma lilowelelepo chifukwa nde zikutiwopsa.
“Nkhanizo zakhala zikupita mabwalo osiyanasiyana koma ngakhale apatsidwe chigamulo, gulu lomwe lidazapempha maloli sililabadira ndipo limapitilira kumanena kuti mfumu Limera ndi anthu ake sakuyenera kukalima kuderako,” watelo munthuyo.
Titayimbira lamya gogo chalo wa delari, mfumu yayikulu Mtumbwinda omwe anabadwa a Franklin Chikwewu Chome, atitsimikizira kuti kangapo konse akhaladi akulandira nkhani ya nkangano wa magulu awiriwa ndipo atawona kuti nawo yawakulira, anakayisiya nkhaniyi m’manja mwa nthambi yowona za malo ku khonsolo ya boma la Machinga.
Mfumuyi yati kumeneko anauzidwa kuti khonsolo ilibe ndalama zoti ingathe kuitanitsa mafumu komaso magulu okhudzidwa kuti akambe nkhaniyi ndipo m’malo mwake mfumuyi inauzidwa kuti ibwelere, ikapemphe mbali ziwirizi kuti zingokhalirana pansi ndikugawana malo akukambidwawo zomwe akuti sizinachitike mpaka lero.
“Ndizowonadi kuti kwa pafupifupi zaka ziwiri, pakhala pali nkangano pakati pa mbali ziwirizi ndipo zinthu zitafika povuta ndinapita ku khonsolo ya Machinga nde kumeneko anandiuza kuti nkhaniyi siyingakambidwe mofulumira chifukwa panopa khonsolo ilibe ndalama.
“Pamene zafika pano, naneso ndamangidwa manja, komatu anthu onsewa ndi a modzi, ndiye nkanakonda anakangokhala pansi ndikugawana malowa kuti anthu a mbali zonse ziwiri azipitiliza kuchita ntchito zawo zaulimi pa malopa,” yatelo mfumu yaikulu Mtumbwinda.
Malingana ndi munthu amene watitsina nkhutu za nkhaniyi, malo omwe magulu awiriwa akulimbirana ndi akulu, mwina kupitilira ma hekitala 10 (more than 100 hectors) ndipo akuti anagawidwa muzidutswa-zidutswa zomwe akaziwerenga sizimachepera makumi anayi (40).