“Watichotsa manyazi” – khamu lakavina ku nyumba kwa Haiya

Advertisement

Zitangodziwika kuti Fleetwood Haiya ndi amene wapambana chisankho cha mtsogoleri wa bungwe la FAM, kunatekeseka ku Ntaja m’boma la Machinga anthu anakhamukira ku nyumba ya mwana wawoyu kukavina kamba kowachotsa manyazi.

Lero loweruka a Haiya apambana chisankho chomwe chimachitika ku bungwe loyendetsa mpira wa miyendo la Football Association of Malawi ndipo iwowa agonjetsa a Walter Nyamilandu Manda ndima voti 23 kwa 13.

Nkhaniyi yadzetsa chimwemwe chodzadza tsaya kwa anthu aku Ntaja komwe a Haiya amachokera kamba koti aka ndikoyamba kuti munthu ochokera m’derali asankhidwe udindo waukulu ngati uwu ndipo zotsatirazi zitangoulutsidwa, kunali mfuwu kudelari.

Pang’onopang’ono anthu anayamba kusonkhana ndipo malikhweru ndi nthungululu zili pakamwa anayamba ulendo opita ku nyumba kwenikweni kwa a Haiya ndipo apapa ndi kuti ng’oma za mganda zitaikidwa paphewa, zikuimbidwa motenga mtima kwinaku anthu akuvina mwa mtima bii.

Malingana ndi kanema wina yemwe akugawidwa m’masamba anchezo, anthuwa atafika ku nyumba kwa a Haiya nde kunali kudumpha ng’oma, kudikula zitenje zitamangidwa mchiuno kwinaku akuimba kuti “Haiya ipemelele, Ipatse moto”.

Chimwemwechi ndi kamba koti akuti kwa nthawi yaitali, dera la Ntaja lakhala likutengedwa ngati dera la anthu omwe sangapite patali komaso ogunata.

Kamba ka chimwemwe ndikupambana kwa a Haiya, malonda anaima kwa mphimdi zochulukirapo pa nsika wa Ntaja kamba koti mdipiti wa anthu ovinawa unakafikaso pa malo ochitira malondawa ndipo pamenepaso panali kudura ziwuno.

A Nyamilandu Manda omwe agonjetsedwa ndi a Haiya, anatenga udindo wa utsogoleri wa bungwe la FAM m’chaka cha 2004 zomwe zikutanthauza kuti akhala pa udindowu zaka khumi mphamvu zisanu ndi zinayi (19).

Advertisement