M’modzi mwa anthu otchuka pa fesibuku, Pemphero Mphande wauza anthu onse omwe akunena kuti mzilazembe pa maimbidwe a Giddes Chalamanda akula asamakaimbe ku ma “show”, kuti ayambe kupeleka ndalama zothandizira umoyo wa tsiku ndi tsiku wa chiyambakaleyu.
Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga nchakuti, lero lachisanu kuyambira 6 koloko madzulo, a Chalamanda akuyenera kukaimba kuphwando la maimbidwe lotchedwa ‘Classic Music Concert’ lomwe lichitikile ku Bingu International Convention Center (BICC) munzinda wa Lilongwe.
Nkhaniyi itangodziwika, kunali kung’ung’udza makamaka m’masamba a nchezo pomwe anthu ambiri akuti sakugwirizana ndi ganizo loti wamvula zakaleyu azipitabe ku ma “show” kukaimba ponena mkuluyu atha kukhala kuti alibe nthanana zoti angaimile mkumaimba kwa ka nthawi.
Koma yemwe akuwatsogolera a Gide, Mphande wati amadabwa kwambiri kuti nthawi zonse iye akamapanga zoti mkuluyu apeze khobidi la sopo kudzera ku ma “show”, anthu m’dziko muno amalubwalubwa kwambiri, kumufooketsa kuti asamugwire dzanja wa mvula zakaleyu.
Mphande wati a Gide akhala akumuuza iye kuti samafuna kungokhala powopa kupha manja komaso powopa kugona ndi njala chifukwa a kuti pakadali pano alibeso njira iliyose yomwe angapange kuti apeze ndalama yogulira chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku.
“Nthawi zambiri ndikapanga post kuti a Giddes ali ndi show, a Malawi ena ake they say akula apumiseni, mukuwakakamiza. I want to address this issue once and for all. Akuluwa anayamba kuimba ine ndisanabadwe. Amakonda kuimba. Ngati ena mumakumbukira pa live inayake mu chaka cha 2021, ndinawafunsa za retirement.
“This is what he said, “ndikapanga retire ndizitani ndipo ndizidya chani?”. Two statements there which are very important. Firstly, he asks, what will I be doing? A Gide anandiuza kuti nthawi yomwe azasiye kuimba azamwalira chifukwa chomwe chawasunga zaka zonsezi ndi music. So who are you to take away from him what he loves?” wadabwa Mphande.
Mphande anapitilira ndikuulura kuti kantini yomwe a Gide anatsegulilidwa zaka zambuyozi, inatha kalekale kotelo kuti pano kuti adye amadalira thandizo kuchokera kwa anthu akufuna kwa bwino zomwe a kuti zamugwedeza iye kuti amukokere mkuluyu kuphwando la maimbidweli kuti akapezeko ya mchere.
Bwezi lake la oyimba Keturah-li lati linayamba m’chakacha 2021 kugwira ntchito ndi a Gide ndipo sakuona vuto kuti mkuluyu aziimbabe ku ma “show” ponena kuti izi ndi zomweso mkulu wa zaka 93 zakubadwayu amasangalatsidwa kuchita ndipo wati anthu onse omwe akufuna kuti bambo ake a Linny asamakaimbe ku ma “show”, ayambe kuwapatsa ndalama ya chakudya.
“Ena akuti akazagwa pa stage ndikumwalira anthu azati mwawapeleka nsembe. Pali nzeru apa? Ngati azafere pa stage akuimba inu muzakondwe kuti munthuyu wafa akupanga zomwe iye amakondwa nazo. Komwe akupitako lero pa 8 December ku BICC kukaimba sindine ndawatuma. Anyamuka okha ndi mwana wawo.
“Ngati mukufuna kuwapumisa, please comment. I will put you in touch with him kuti muziwapasa ndalama pa mwezi to survive. Ngati simungapeleke ndalama ndisazamveso mfwe mfwe. Fotseki!” wang’alura Mphande.