Aliyense atengepo mbali polimbana ndi ziphuphu ndi katangale – Chizuma

Advertisement
Martha Chizuma in Balaka

Mkulu wa bungwe lolimbana ndi kuthana ndi mchitidwe wa ziphuphu komanso katangale  la Anti-corruption Bureau, mai Martha Chizuma, ati ndi kofunika kugwirana manja kuti dziko lino lipambane pa nkhondo yolimbana ndi mchitidwe oipawu.

A Chizuma amayankhula izi dzulo pomwe bungwe la ACB mogwilizana ndi khonsolo ya boma la Balaka linakonza mwambo osesa komanso kuchotsa zinyalala mu msika waukulu wa pa boma la Balaka.

Iwo adati ndi kofunikira kwambiri kuti aliyense atengepo gawo pomenya nkhondo yolimbana ndi mchitidwewu.

Ndipo lero, nthambi ya ACB ikuyembekezera kuchititsa mwambo ophunzitsa anthu za kuipa kwa mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale kudzera pa galimoto ya chimkuzamawu ndipo mwambowu ukuyembekezeka kuzayambira ku Mpale.

Izi zikudza pamene nthambi ya ACB ikhale ikukondwelera zaka 25 chilikhadzikitsileni mdziko muno komanso ngati mbali imodzi yokumbukira kuthana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale padziko lonse la International Anti-corruption Day)omwe uchitike loweluka likudzali ku Balaka.

Advertisement