Zigoli 7 za Moyale Barracks zatutumutsa anthu, Blue Eagles yakamang’ala

Advertisement
Super League Malawi football side Moyale Barracks

Timu ya Moyale Barracks yomwe imafunika kugoletsa zigoli zisanu ndi ziwiri (7) kuti isawonetsedwe nsana wa njira muligi yaikulu ya TNM, yadabwitsa anthu pomwe inakwanitsa kuchinya zigoli zonsezi pomwe imasewera ndi timu ya Red Lions ndipo timu ya Blue Eagles ikuganiza kuti panayenda chinyengo ndipo yakasuma.

Kunali mpira wa magazi la Mulungu lapitali pomwe ma timu a Silver Strikers, FCB Nyasa Big Bullets komaso Mighty Mukuru Wanderers amalimbirana akatswiri wa ligi yaikulu m’dziko muno ya TNM, koma pamapeto pa zonse zinakomera timu ya Bullets yomwe yatenga ukatswiriwu kachisanu motsatizana.

Pomwe njovuzi zimalimbirana ukatswiriwu, nawo ma timu angapo kuphatikizapo Moyale Barracks komaso Blue Eagles, nawo analumira milomo pomwe amafuna kudziteteza kutuluka mu ligiyi koma pakutha pa zonse zinakomera timu ya Moyale pomwe a kuti ndi yomwe yapulumuka ku chigwa cha imfachi.

Koma kupulumuka kwa timu ya Moyale Barracks yomwe ndi ya asilikali okhaokha, kwadzetsa manong’onong’o kamba koti zodabwitsa zachitika pomwe timuyi inakwanitsa kuchinya timu ya Red Lions zigoli zonse zisanu ndi ziwiri (7) zomwe zimafunika kuti zipulumutse timuyi kutulutsidwa mu ligi ya TNM.

Anthu ena makamaka m’masamba anchezo ati akawona kanema yemwe akuyenda m’masamba anchezo yemwe akuonetsa momwe timu ya Moyale imachinyira zigoli zake pa tsikuli, ati akuona ngati panayenda zachinyengo kwambiri pa masewerowa.

“Kungowona zigoli zakezo, munthu utha kudziwiratu kuti pali march fixing. Komano izi ngati sitisamala zitha kutionongera mpira m’dziko muno. Ine ngati nzika yokhudzidwa mkanakonda Sulom inakakhazikitsa kafukufuku pa nkhaniyi, aaa sizowona izi,” anatelo munthu wina yemwe anaikira ndemanga pa tsamba lathu la fesibuku atawonera kanema wa zigoli zomwe timu ya Moyale inachinya.

Chimene chadabwitsa anthu kwambiri nchoti timu ya Red Lions inatulutsa m’masewerowa katswiri wawo oteteza golo Nenani Juwaya pomwe anachinyitsa chigoli chimodzi chokha kudzera pa penate ndipo m’malo mwake munalowa Precious Mitolo yemwe adagoletsetsa zigoli zisanu ndi chimodzi (6) mgawo lachiwiri.

Potsatira izi, timu ya Blue Eagles yomwe akuti yatuluka mu ligiyi kutsatira kugonja kwake ndi timu ya Mafco komaso kutsatira kupambana kwa Moyale, yakagwada ku bungwe la Super League of Malawi kulipempha kuti lifufuze bwino za kupambana kwa timu ya Moyale Barracks ndi zigoli zonse 7 zomwe zimafunikira.

Timuyi kudzera kwa mlembi wake wa mkulu a Benjamin Msowoya, wauza nyumba ina yofalitsa nkhani m’dziko muno kuti akuganiza kuti panachitika za chinyengo pa masewerowa ponena kuti ndizodabwitsa kuti m’mene ilili timu ya Moyale ikachinye timu ya Red Lions zigoli zisanu ndi ziwiri.

Kupatula apo, a Msowoya ati timuyi yakamang’alaso kamba koti ndiyodabwa kuti Blue Eagles yatulutsidwa mu ligi ya TNM pomwe ikufanana chilichonse ndi timu ya Moyale Barracks komaso ati akudandaula kuti yemwe anaimbira masewero omwe imamenya ndi timu Mafco, anawakanira chigoli.

“Takadandaulaso za ganizo la yemwe anaimbira masewero athu omaliza ndi timu ya Mafco yemwe anatikanira chigoli chomwe timu yathu inachinya chowoneka ndi maso bwino bwino,” watelo Msowoya.

Pakadali pano bungwe la Sulom kudzera kwa mlembi wake a Williams Banda ati awunikira dandaulo la timu ya Blue Eagles koma anenetsa kuti malamulo akuyeneleka kutsatidwa nthawi zonse.

Malingana ndi malamulo a bungwe la Sulom, timu ya Blue Eagles yatulutsidwa mu ligi ya TNM kamba koti ngakhale timu yake inafanana mphamvu ndi timu ya Moyale Barracks, Eagles inagonja komaso kulepherana mphamvu ndi timu Moyale m’masewero ake awiri amuligiyi chaka chino.

Advertisement