A Jeffrey akubweretsa chisokonezo ku DPP, watero Msaka

Advertisement
Democratic Progressive Party press conference

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) wa chigawo cha ku m’mawa a Bright Msaka wati zomwe aanchita mlembi wachipanichi  Grezeldar  Jeffrey poitanitsa msonkhano wa komiti yaikulu yoyendetsa DPP opanda chilolezo cha pulezidenti wachipanichi ndikupeputsa mtsogoleri was DPP a Peter Mutharika komanso kubweretsa chisokonezo.

A Msaka anena izi pa msonkhano omwe unachitika lolemba ku  Lilongwe.

Iwo adati chipani chimayenera kulemekeza mtsogoleri wake chifukwa munthu sangangodzuka kwawo nkuyamba kupanga zinthu payekha chifukwa chipani sichiyenda ndi munthu m’modzi.

“A Malawi tonse komanso osatira chipani cha DPP mukudziwitsidwa kuti  pa 6 December chaka chino kulibe msonkhano wa National Governing Council (NGC). Mau amenewa andituma ndi a pulezidenti Peter Mutharika. Choncho tiyeni patsikuli tidzapite ku ntchito kaya kolima potengera kuti nthawi ino ndiyolima. Tsiku la NGC likakonzedwa aliyense adzafotokozoredwa. Mtima ukhale m’malo aliyense, DPP ikukonza zinthu ncholinga choti 2025 tilowe m’boma ndikuphura a Malawi pamoto omwe akukumanawo padakali pano,” adatero a Msaka.

Pothirirapo ndemanga, oyankhulila chipanichi a Shadreck Namalomba adati msonkhano wa NGC umayenera kuitanitsidwa ndi komiti yaikulu ya Central Executive Committee ya chipani komanso mlembi ndi pulezidenti amayenera  kuunika zina ndi zina kenako nkusankha tsiku lodzapangira msonkhanowu.

A Namalomba anati ngati chipani akuyenera kudekha bwinobwino kuti nkumano wawo odzasankha maudindo atsopano mchipani udzayende bwino.

Iwo apempha anthu otsatira chipani cha DPP kuti akhale ochenjera ndi anthu omwe akufuna kubweretsa kusamvana pakati pawo chifukwa iwo sakudziwa cholinga chawo chenicheni.

Sabata yathayi Mlembi wachipanichi a Jeffrey anapangitsa msonkhano wa atolankhani komwe anati chipani cha DPP chikhala ndi msonkhano waukulu pa 6 December.

Advertisement