Bambo wa zaka 32 wafa atagundidwa ndi sitima ku Machinga

Advertisement
Railway line in Machinga in Malawi

Bambo wa zaka 32 yemwe dzina lake ndi Ashan Khalima wafa atagundidwa ndi sitima yapamtunda ku Machinga.

Mkulu wa a Police Boma la Machinga Senior Assistant Commissioner Jane Mandala watsimikidza zangoziyi poyankhula ndi Malawi24.

A Mandala ati ngoziyi idachitikira mdera lotchedwa Mphonde cha m’ma 10 koloko usiku pafupifupi makilomita 14 kuchokera ku Nayuchi Railway Station.

Iwo ati m’bale wa malemuwa a Henry Chabwera ndi womwe adakadziwitsa a police zakugundidwa kwa Ashan Khalima.

Assistant Commissioner Mandala akuchenjedza anthu a Boma la Machinga kuti asamakonde kucheza kapena kuyenda mu njanji ya sitima pofuna kupewa ngozi.

Pakali pano thupi lamalemuwa akulisunga kuchipatala chachikulu cha Boma la Machinga kudikilira kuti abale  ake adzalitenge kupita nalo kumudzi kwao.

Malemu Ashan Khalima alindi zaka 32 ndipo amachokera mudzi mwa Nkata, T/A Mwambo, Boma la Zomba

Advertisement