A Malawi ali nafe chikhulupiriro — DPP

Advertisement
Malawi Politics

Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chati kuchoka kwa mamembala a zipani zina omwe akuti alowa mu chipani cha DPP ndi chitsimikizo chakuti nzika zambiri za dziko lino zili ndi chikhulupiriro ndi chipani cha DPP.

Gavanala wa chipanichi ku chigawo cha kum’mawa, Sheikh Emran Mtenje amayankhula izi dzulo ku Balaka pamene amalandira anthu okwana 76 omwe akuti achoka ku chipani cha United Front komanso munthu mmodzi yemwe akuti wachoka ku chipani cha UTM.

A Mtenje adawonjezeranso kunena kuti posachedwapa akhala akulandira ma membala ena omwe atuluka chipani cha Malawi Congress (MCP).

Koma poyankhapo ngati kubwera kwa anthuwa kukhale ndi phindu lililonse ku chipani cha DPP potengera kuti anthu ena amazitenga zipanizi kukhala ngati banja limodzi, a Mtenje adafotokoza kuti kubwera kwa anthuwa ndi kofunikira kwambiri ndipo kulimbikitsa kagwilidwe ntchito mu chipani cha DPP.

“Kunena kuti zipani za DPP komanso UDF ndi banja limodzi ndi kulakwitsa kwambiri,” adatero a Mtenje.

Iwo adawonjezera kunena kuti zipanizi ndi magulu awiri osiyana ngakhale kuti nthawi zina amagwilira ntchito limodzi pakafunika kutero.

“Ubale wathu ndi chipani cha UDF umatha kukhalapo panthawi ya chisankho komanso ngati pali ntchito yoti tigwilire limodzi ku nyumba ya malamulo.Mutha kuona kuti aliyense ali ndi makaka ake, zomwe zikusonyeza kuti ndife zipani ziwiri zosiyana,” a Mtenje adafotokoza.

A Greyton Mike Chimenya ndi m’modzi mwa anthu omwe akuti alowa mu chipani cha DPP kuchokera ku UDF.

Iwo akuti aganiza zolowa chipanichi kaamba ka mfundo zabwino zomwe chipanichi chimatsatira. A Chimenya adatinso amasunthika ndi utsogoleri wa luntha komanso kupanda tsankho omwe mtsogoleri wa chipani cha DPP, Arthur Peter Mutharika ali nako.

Koma poyankhapo pa nkhaniyi, mneneri wa chipani cha UDF a Yusuf Mwawa ati iwo angomvetsedwa kudzera mu masamba a mchezo apa intaneti kuti anthu ena achoka ku chipanichi. Komabe, a Mwawa ati izi sizoona.

“Anthu amene akunenedwawo ndi mamembala kale a chipani cha DPP ndipo sadakhalepo ma membala a chipani cha UDF,” adatero a Mwawa.

Iwo adafotokoza kuti chipani cha DPP chikupanga izi powopa chipani cha UDF.

Pothilira ndemanga ngati pakali pano pali ubale pakati pa zipani ziwirizi, a Mwawa adati sangafotokoze zambiri pakuti ubale wawo udali okhudza masankho a mchaka cha 2019.

Advertisement