Akuluakulu aboma ati ngakhale msonkhano omwe umayenera kuchitika m’dziko la Saudi Arabia walepheleka, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anyamukabe lero masanawa kupita m’dzikolo.
Lachiwiri sabata ino boma linalengeza kuti a Chakwera anyamuka lero Lachitatu kupita m’dziko la Saudi Arabia komwe akakhale nawo pa nkumano wa mayiko a mu Africa komaso maiko anchigawo cha ku m’mawa (middle east) omwe ukutchedwa ‘Africa-Arab Summit’.
Koma patangotsala maola ochepa kuti a Chakwera anyamuke kumapita m’dziko la Saudi Arabia, akuluakulu omwe amayendetsa zokonzekera msonkhano wa Africa-Arab Summit, alengeza kuti nkumanowu wayamba wayimitsidwa kaye.
Malingana ndi nyumba zina zofalitsa nkhani zakunja, kuyimitsidwa kwa msonkhanowu omwe umayenera kuchitika pa 10 ndi 11 November, 2023, ndi kamba ka mpungwepungwe omwe uli kudera la Gaza m’dziko la Palestine pakati pa dziko la Israel ndi gulu la Hamas.
Ngakhale sanatchule tsiku lenileni, akuluakulu a dziko la Saudi Arabia ati nkumanowu omwe umayenera kuchitikira ku dera la Riyadh ukhalapo kutsogoloku koma ati ndikofunikra kuti nkumanowu usasokonezedwe ndi nkhondo yomwe yabukayo.
Koma ngakhale msonkhanowu walepheleka, nduna yofalitsa nkhani m’dziko muno a Moses Kunkuyu, ati Chakwera akhala akunyamukabe masana ano ngati momwe anakonzera poyamba kupita ku Saudi Arabia.
A Kunkuyu awuza atolankhani m’dziko muno kuti nkumano omwe a Chakwera akunyamukira lero siwomwe waimitsidwa koma ati ndiomwe apatsidwa ndalama ndi banki ya Saudi Development yomwe ikhalenso ikupeleka ngongole yopitilira 2.2 biliyoni kwacha ku dziko lino kuti limangile msewu wa Mangochi-Makanjira.
“Uwu ndi nsonkhano omwe ndi ofunika kwambiri komwe akukasaina pangano lomanga nsewu wa Mangochi-Makanjira. M’nthawi yomweyi, a President Dr Lazarus Chakwera akuyeneranso kupita nawo kumsonkhano wa Saudi – Africa summit.
“Msewu wa Mangochi-Makanjira wokwana madola 20 miliyoni (pafupifupi K24 biliyoni) udzathandizidwa ndi bungwe la Saudi Fund for Development lomwe ndi bungwe la boma la Saudi Arabia lomwe limapereka thandizo lachitukuko ku mayiko omwe akutukuka kumene monga dziko la Malawi popereka ndalama zoyendetsera ntchito zachitukuko ndi chitukuko.
“Izi sizili pansi pa Arab-Africa Summit kapena Arab League. Choncho, ulendo wa Pulezidenti ndi kamba ka ubale wa Saudi-Malawi ndipo kulepheleka kwa msonkhano wa Arab-Africa Summit sikusintha kanthu chifukwa sikungakhudze ntchito yofunika yomwe pulezidenti akuyenera kukagwira,” adatero Kunkuyu.
A Chakwera akuyenera kunyamuka pa bwalo la ndege la Kamuzu International munzinda wa Lilongwe lero nthawi ya 14:25 ndipo akuyembekezeka kubwerera kuno kumudzi Lachiwiri pa 14 November, 2023, nthawi ya 13:35.
Kupatula kupita m’dziko la Saudi Arabia, a Chakweraa kukakhala nawo pa chiwonetsero chachitatu cha zamalonda Africa chotchedwa Intra-African Trade Fair (IATF2023) chomwe chichitikire ku Cairo m’dziko la Egypt kuyambira pa 13 November, 2023.
Akuluakulu a boma alengezaso kuti maulendo awiri onsewa, a Chakwera akuyenera kunyamuka ndi anthu osachepera 70 omwe ndikuphatikiza nthumwi za makampani osiyanasiyana komaso akuluakulu a boma.