Apolisi atatu ayimitsidwa ntchito kamba ka chamba

Advertisement

Apolisi okwana atatu omwe amagwira ntchito pa police ya Nkhunga m’boma la Nkhotakota, ayimitsidwa ntchito ndi nthambi ya chitetezo ya Malawi Police kamba kokhudzidwa pa nkhani yogulitsa chamba.

Kuyimitsidwa ntchitoku kwadza pamene a polisiwa adapezeka okhudzidwa kuti iwo adagulitsa chamba cha makilogalamu ochuluka omwe adalanda kwa mkulu wina m’boma lomwelo.

Apolisiwa adamangidwa ndipo akuyankha mulandu ogwiritsa ntchito mphamvu za ofesi yawo molakwika zomwe ndizosemphama ndi lamulo 95 la malumolo a dziko lino.

Apolisi omwe ayimitsidwa ntchitowa ndi Sub-lnspector Milward Chakumanika, lnspector Nelson Gulani ndi Sergeant Robert Kapalamula.

Malingana ndi uthenga omwe asayinila ndi a Maxton Kalimanjira omwe ndi owona za ogwira ntchito ku polisi, apolisiwa sazipita ku ntchito koma azilandira malipiro awo.

Wolemba: Ben Bongololo Gondwe

Advertisement