Zeze sanandilande Dorothy Shonga – watelo Blakjak

Advertisement
Dorothy Shonga with her boyfriend Zeze. The two are set to get married in 2024

Oyimba nyimbo za dancehall Blakjak wakanitsitsa mwa ntu wa galu mphekesera zomwe zakhala zikumveka zoti analandidwa Dorothy Shonga ndi Zeze Kingstone

Blakjak yemwe anabadwa Fatsani Che Kalonda amayankhula izi pomwe amacheza ndi kanema ina ya nsangulutso pa masamba anchezo sabata yatha.

Mkati mwa kucheza, Blakjak anatsindika kuti iye ndi Dorothy Shonga anali pa chinzake chabe ndipo panalibe malingaliro achibwenzi pakati pawo monga momwe anthu ena akhala akukambira.

Poti khoswe wa patsindwi anawulura wapadzala, Blakjak yemwe anatchuka ndi nyimbo ya ‘Wadya Iwe’, anawulura kuti zomwe wakhala akulemba pa m’masamba ake anchezo kuti Dorothy ndi ma hope ake inali mbali imodzi ya bizinezi pakati pa awiriwa.

“Anthu ambiri amaona ngati Zeze anandilanda mkazi, sanandilande mkazi. Dorothy Shonga ndiine tinali pa chinzake china chake chochezana nkumanenana kuti ma hope anga, ma hope anga.

“Ndipo akafuna kupanga promote china chaka amabwera kwa ine. Nde tinkamagwiritsa ntchito zomanenana kuti ma hope kuti apange promote chinthu china chake monga nyimbo,” anatelo Blakjak.

Che Kalonda anati kuyitanizana kuti mahopu ndi Dorothy Shonga kunafika pamlingo wina pomwe mzimayiyu anayamba kuyankha mlandu okhudza ndalama zaka ziwiri zapitazo ndipo wati pa nthawiyi, ankafuna kuti anthu achepetse kumutoza mzimayiyu zokhudza mlanduwo.

Potsindika kuti awiriwa sanali paubwezi, oyimbayu anati sanamufusilepo Dorothy ndipo wati atadziwa kuti Zeze akuzembelera nkaziyu, anasiya zomamutchula kuti ma hope.

“Tsiku lomwe Zeze anabwera ndinali ndi Dorothy ku Amaryllis Hotel usiku, ndipo nditabwelera, mmawa ndinawona zithunzi za Zeze ndi Dorothy ndipo kenaka ndinamuimbira Zeze kumufusa kuti zithunzi izi sizawamba, tandiuza chenicheni chomwe chikuchitika.

“Nde ndinamuuza kuti ineyo mkaziyu ndimacheza naye koma apapa ndikuona ngati ndichepetse chifukwa iweyo waonetsa chidwi pa mkaziyu. Nde ine ndi Zeze tinagwirizana kuti ineyo ndisiya zomukamba Dorothy kwambiri kuti iyeyo akhale ndi mpata wambiri,” anawonjezera choncho Che Kalonda.

Blakjak wati atasiya kukamba kwambiri za Dorothy anayamba kukamba kwambiri za Wendy Harawa chifukwa nayeso ankafuna amupange promote kuti nyimbo zake zidzikondedwaso kuno ku Malawi osati kunja kokha.

Advertisement