Ophunzira ku Mzuni abwelera kusuluku sabata lamawa

Advertisement
Mzuzu University

Ophunzira apa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University (Mzuni) awauza kuti abwerele ku sukulu Lolemba pa 23 October.

Izi zadza kutsatira chikalata chomwe sukuluyi yatulutsa mmawa wa lero.

Sukuluyi yakana kutsitsa mitengo ya tsopano ya fizi yomwe idapangitsa kuti ophunzirawa achite zionetsero pofuna kuti mitengoyi itsike ndikuti mitengo yatsopanoyi idzayambe kugwira ntchito akamadzayamba chaka chatsopano.

Mwazina, chikalatachi chati ophunzirawa adzayenera kusayinira ma fomu akadzafika pa sulukopo.

Sukuluyi yakananso nkhani yokhudza kafukufuku yemwe adaonetsa kuti ophunzirawa adaononga katundu wa ndalama zokwana K93 miliyoni.

Ophunzirawa akhala ali kunyumba pafupifupi mwezi umodzi potsatira zionetsero zomwe zidachitika pa 16 September zomwe zidapangitsa kuti sukuluyi atseke.

Wolemba: Ben Bongololo Gondwe

Advertisement