Uja amatamika ndi za mafuta ngambwi ngambwi ali kuti? Chifukwa tsopano akuyenera kupepesa a Malawi, azingoyenda ali werawera. Mkulu wa bungwe la MERA a Henry Kachaje ati za mafuta ngambwi ngambwi ndi zoduka mutu, posachedwapa tionanso mizere ija.
Polankhula ku bungwe loyang’anira za mphamvu ndi kusintha kwa nyengo la nyumba ya malamulo, a Kachaje ati dziko lino liri pachiopsezo choonanso kadamsana wa kusowa kwa mafuta maka chifukwa cha kunyanyala ntchito kwa oyendetsa ma thankala onyamula mafuta.
Akuluakulu oyendetsa galimotozi ati iwo ndi okwiya ndi malipiro ochepa amene amalandira kudzanso kusakondwa ndi kuvutika kuti apeze ziphaso zoyendera (passport) ndi mavuto ena. Iwo akhala akunyanyala ntchito kuti boma likonze mavutowa.
Pounikilapo vuto la kunyanyala kumeneku, a Kachaje ati ngati kusamvana uku sikutha mwachangu, kapezekedwe ka mafuta kakhudzidwa. Iwo ati pakali pano nkhokwe za mafuta sikuti muli kanthu kenikeni ndipo dziko lino likudalira akuluakuluwa kuti akhale akuyendetsa mafuta akagulidwa kukawafikitsa ku ma filling station.
A Kachaje aonjezeraponso kuti vuto la mafuta lipitilira chifukwa tsopano dziko la Malawi lidakapitilira kusowa ndalama za maiko akunja. Iwo ati pa Mwezi, mafuta okha akumafuna 60 miliyoni dollars koma pena kukumapezeka 40 miliyoni yokha, pena ngakhale 20 miliyoni yeniyeni.
Ati izi zikuika pa chiopsezo kapezekedwe ka mafuta.