Harris Jaspar Kasambara tsopano ndi Mr Zomba

Advertisement
Harris Jaspar Kasambara is the reigning Mr Zomba in Malawi

Harris Jaspar Kasambara tsopano ndi Mr Zomba atagonjetsa anzake ena asanu ndi anayi (9) pamasewero a olimbitsa minyewa omwe adachitika pa Jokala Club mu boma la Zomba ndipo pokhala katswiri walandira ndalama zokwana 120,000 kwacha.

Kasambara yemwe ndi msilikali wa Police kunthambi ya PMS ku Police College ku Zomba, wati chinsinsi chake chidagona polimbikira kuchita zokonzekera ndipo adathokoza anthu omwe adabwera kudzamuchemelera.

Iye wati pakali pano akufunitsitsa kutsogoloku atadzapikitsana nawo masewero a Mr Malawi ndikudzatenganso ukaswiri.

“Ndithokoze anzanga onse omwe ndapikitsana nawo chifukwa andipatsa masewerowo abwino popedza nawonso adakonzekera bwino kwambiri,” adatero Harris Jaspar Kasambara.

Poyankhula atatha  masewerowo, a Bright Limani omwe adakonza mpikisano wa Mr Zomba adati ndiwokhutitsidwa ndimomwe mpikisanowo wayendera komabe adadandaula chifukwa chokusowa kwa anthu komanso ma company othandidza.

A Limani adati mtsogolo muno akufunitsitsa atadzachititsa masewerowo a Mr Eastern Region pofuna kupititsa patsogolo masewerowo olimbitsa thupi.

Iwo adapempha ma company komanso anthu okufuna kwabwino kuti abwere poyera ndikuyamba kuthandidza masewerowa.

Advertisement