Yawo ija angoni: fisi wapangidwa ndiwo ku Ntcheu

Advertisement
A hyena was killed in Ntcheu and prepared for food

Sadyeka uja lero wadyeka: Angoni a ku Ndagoma m’boma la Ntcheu adodometsa gulu pomwe achita ndiwo fisi yemwe wakhala akuwathera mbuzi m’mudzimo.

Izi ndi malingana ndi kanema ina yomwe anthu akugawana m’masamba a mchezo yomwe ikuwonetsa azibambo angapo akuwawura fisi yemwe anamupha m’bandakucha wa lolemba pa 2 October.

Izi zachitika m’mudzi wa Ndagoma omwe uli mphepete mwa nsewu wa M1, omwe unayandikana ndi sukulu ya Kings Foundation ndipo mudziwu uli mtsindetsinde mwa phili la Ntcheu.

Malingana ndi kanemayu, chilombochi monga mwa nthawi zonse chinatsetseleka kuchoka mphili ndikulowa m’mudziwu kuti chikasake zakudya ndipo mphuno salota, chinakadziwa sichikanapanga chibwana cha nchombo lende ngati chimenechi.

Poti mphuno salota, mkati mosaka zakudya zake, fisiyu anafika pa nyumba ina komwe anagwera mudzenje lina lomwe akuti lakumbidwa kuti likhale mofikira nyasi zochokera m’nyumba yodzithandizira.

Mphavu zachilombochi sizinaphule kanthu kuti chituluke mdzenjeli kufikira m’bandakucha pomwe chinakumana maso ndi maso ndi angoni ankhuliwa.

Malipoti akusonyeza kuti m’ma 4 koloko m’mawa munthu wina anapeza fisiyu ali wefuwefu, diso lili pantunda akukanika kutuluka mdzenjeli ndipo anaitana ena ndikutulutsa mipaliro ndi mauta ndikuyamba ntchito yopha chilombochi.

Fisiyu ataphedwa anthu ena amaona ngati atayidwa ndipo apa mpomwe azibambo ena anayamba kusonkhanitsa mapesi kuti awaule ndi kuchita ndiwo fisiyu.

Munkanema yomwe anthu akugawana m’masamba anchezoyi, ikuwonetsa azibambowa akumupala fisiyi, kochotsa ubweya ndipo akatelo akuyenera amuduledule ndikumugawana kuti aliyese akadyeko ndiwo yonona.

Boma la Ntcheu ndilimodzi mwa maboma omwe kuyambira pakanthawi amadziwika kuti ali ndi chiwerengero chochuluka cha a fisi.

Advertisement