Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra) latsindika kuti ntchito yomwe bungweli ikugwira poika zizindikiro komanso zikwangwani mu malo osiyanasiyana (National Addressing System) sikugwilizana ndi pang’ono pomwe ndi chisankho cha pulezidenti, aphungu akunyumba yamalamulo komanso ma khansala chomwe chikuyembekezeka kuchitika mdziko muno mu chaka Cha 2025.
M’modzi mwa akuluakulu ku bungweli, a Burnet Namacha, ndiwo anena izi pa mkumano omwe bungweli lidakonza pofuna kudziwitsa akuluakulu a khonsolo ya Balaka komanso magulu ena osiyanasiyana m’bomali.
Poyankhapo pa nkhawa yochokera kwa khansala wa wodi ya Shire m’bomali, a Dickson Wasili, a Namacha adati bungwe la Macra silikhudzidwa pakayendetsedwe ka chisankho.
Khansala Wasili adafuna kudziwa makamaka ngati ntchito yoika akalozerayi ingakhale ndi kuthekera kosokoneza zotsatira za chisankho potengera kuti bungwe la Macra mwazina lidzigwilitsa ntchito zitupa za unzika (National Identity Cards) pogwira ntchitoyi.
Koma a Namacha adatsimikizira a Malawi kuti asakhale ndi nkhawa iliyonse popeza kuti ntchitoyi idayamba zaka zammbuyomu.
“Monga mukudziwira, Ife a Macra tidayamba kugwira ntchitoyi moyesera (pilot) mu chaka cha 2017 ndipo kufikira lero taphunzirapo zinthu zingapo zomwe zitithandizire kuti ntchitoyi iyende bwino monga mwa ndondomeko yake,” adatero a Namacha.
Pothilirapo ndemanga pa ntchitoyi, mkhalapampando wa khonsolo ya Balaka a Osman Mapira adayamikira bungwe la Macra kaamba ka ntchitoyi ndipo adalonjeza kutengapo gawo pothandizira kuti ntchitoyi igwilike mwa ndondomeko yake.
Malingana ndi bungwe la Macra, ntchitoyi ikadzatha idzathandizira kupititsa patsogolo ntchito zosiyanasiyana monga za kalembera wa anthu, ntchito zokopa alendo komanso kulimbikitsa chitetezo cha mdziko ndi zina zambiri.