Ophunzira ku Unima akuganiziridwa kuti ali ndi Cholera ku Zomba

Advertisement

A zaumoyo ku Zomba ati ophunzira wa ku sukulu ya ukachenjede ya Unima wagonekedwa mchipatala ku Zomba ndipo akuganiziridwa kuti ali ndi Cholera.

Malingana ndi a Arnold Mndalirs omwe amayankhulira ofesi ya za umoyo ku Zomba, ophunzirayu yemwe amakhala ku Chikanda akuganiziridwa kuti ali ndi nthenda ya cholera.

Pakali pano azachipatala amuyesa ndipo zotsatira zikuyembekezeka Kutuluka pakadutsa maola 24.

A Mndalirs apempha kuti apewe kutaya matewera palipomse poti ndi njira imodzi yomwe imafalitsa nthenda ya Cholera.

Nthenda ya Cholera inavuta ku Malawi kwa chaka, kuyambira mu March chaka Cha 2022 kufika mu February chaka chino.

Anthu okwana 58,982 anapezeka ndi Cholera mu nthawiyi ndipo 1,768 anamwalira kamba Ka nthendayi.

Advertisement