Asilamu atentha dambwe ku Kasungu

Advertisement
Dambwe laotchedwa

Asilamuwo atentha dambwe m’mudzi wa Mchinga kwa mfumu Njombwa ku Kasungu chifukwa gule wamkulu anagwira mwana wa mtsogoleri wachisilamu kukalowa naye ku dambweko.

Malingana ndi wailesi ya Zodiak, gule wamkulu anagwira mwana wa mtsogoleri wachisilamu kukalowa naye ku dambweko ndipo izi ndi zomwe zinayambitsa mkangano pakati pa magulu awiriwa.

A Paul Dickson omwe anaona izi zikuchitika auza Zodiak kuti bambo wa mwanayo anagwidwanso ndi guleyo dzulo pomwe amakatenga mwana wakeyo ati chifukwa choti anamenya m’modzi wa guleyo.

Pokwiya ndi zochitikiza, asilamu anapita ku dambwe Konko komwe ndi ku manda ndipo anakatengako mwana ndi bamboyo yemwe ndi Shehe.

Asilamuwo anatenthanso dambwe la gule wamkuluyo.

Padakali pano, Mfumu Njombwa yadabwa ndi zochitikaza gule wamkulu potengera mwana ku dambwe poti chipembedzo cha chisilamu sichilola mamembala ake kulowa gule.

Advertisement