Pasapekeze ogulitsa mafuta mu zigubu — yatero MERA

Advertisement
Fuel

Pamene mafuta agalimoto akupitilira kusowa m’dziko muno, bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lati anthu onyamula zigubu asaloledwe kugula mafuta pamalo omwetsera mafuta.

Mu chikalata chomwe yatulutsa, MERA yati anthu ena akumagula mafuta ambili mu zigubu ndi cholinga chokuti akagulitsenso mafutawo pa mtengo okwera zomwe zikupangitsa kuti mafuta azipitilira kusowa.

Malingana ndi bungweli, kugulitsa mafuta mu chigubu opanda chilolezo cha MERA ndi kosaloledwa.

Bungweli lachenjezanso oyendetsa malo omwetsera mafuta m’dziko muno kuti asagulitse mafuta mokwera mtengo potengera mwayi kusowa kwa mafutawa.

Mtengo wovomerezeka wa petulo ndi K1,746 pa lita ndipo wa dizilo ndi K1,920 pa lita koma ena akumagulitsa K5000 pa lita.

MERA yati malo omwetsera mafuta omwe apezeke akugulitsa pa mtengo wokwera kapena kugulitsa mafuta kwa onyamula zigubu adzalandidwa zilolezo zochitira malonda ogulitsa mafuta.

Advertisement