Atolankhani adandaulidwa pakusavala bwino

Advertisement

Bungwe la Media Council of Malawi (MCM) lati likulandira madandaulo ochuluka pa nkhani yakusavala moyenera kwa ogwira ntchito zofalitsa nkhani mdziko muno.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe bungwe la MCM latulutsa lero lolemba pa 3 August, 2023 chomwe asayinira ndi a Moses Kaufa komaso a Wisdom Nelson Chimgwede omwe ndi ena mwa akuluakulu a bungweli.

Media Council of Malawi yati anthu ochuluka kuphatikazapo akuluakulu a nyumba ya malamulo komaso akuluakulu a ku nyumba ya chifumu, akamang’ala ku bungweli pakhalidwe la kusavala bwino kwa ina mwa ogwira ntchito zofalitsa nkhani.

Apa bungweli lakumbutsa ogwira ntchito zofalitsa nkhani onse mdziko muno za kufunika kovala moyenera makamaka pomwe akupita kukagwira ntchito yawo mmalo osiyanasiyana.

“Media Council of Malawi yalandira madandaulo kochokera kwa anthu okhudzidwa osiyanasiyana omwe ndikuphatikizapo akuluakulu a nyumba ya malamulo komaso akuluakulu a nyumba ya chifumu pa kavalidwe ka ogwira ntchito zofalitsa nkhani komwe kakumakhala kosagwirizana ndi zochitika za kumalo omwe apita.

“Choncho, MCM ikufuna kukumbutsa ogwira ntchito zofalitsa nkhani ndi anthu onse okhudzidwa za gawo 2.1 la Media Code of Ethics and Professional Conduct, yomwe imanena kuti mtolankhani azivala zovala zoyenerana ndi mwambo komaso malo omwe wapita kukagwira ntchito,” chatelo chikalata cha MCM.

Bungweli lati kuvala bwino kwa atolankhani kungathandizire kusunga mbiri yabwino ya ntchito ya utolankhani komaso lati zitha kuthandiza kuti ntchito ya utolankhani izipatsidwa ulemu.

Ngakhale zili choncho, bungwe la MCM lauza magulu amene akudandaula za mavalidwe osayenelawa kuti nthawi zina ogwira ntchito zofalitsa nkhani amavala molingana ndi ntchito yomwe akukagwira tsiku limenelo.

“Momwemonso bungwe la MCM likukumbutsa anthu odandaulawa kuti kavalidwe ka ofalitsa nkhani kamatengeraso ntchito zomwe akugwira tsiku limenelo, poganizira kuti ena ndi akatswili a za tekiniko (technical) ndipo amayenera kuvala zomwe zingawapangitse kugwira bwino ntchito.

“Choncho, nyumba zofalitsa nkhani zimalimbikitsidwa kuti ziwonetsetse kuti ogwira ntchito za tekiniko ali ndi kavalidwe koyenera,” yatelo mbali ina ya chikalatachi.

MCM yalimbikitsanso ogwira ntchito zofalitsa nkhani kuti azinyamula zitupa zawo akamagwira ntchito komaso yauza anthu kuti adzilitsina khutu akaona kuti mtolankhani wina wachita zonyazitsa ntchito ya utolankhani.

Advertisement