Lucius Banda wang’alura Pop Young powulura mitengo yake

Advertisement
Lucius Banda wang'alura Pop Young powulura mitengo yake

Chiyamba kale pa mayimbidwe, Lucius Banda, wadzudzula oyimba mzake Pop Young kaamba koyika pa mbalambanda mitengo yomwe amatchaja akayitanidwa kukaimba ku malo osiyanasiyana.

Nkhaniyi ikudza pomwe posachedwapa Pop Young yemwe anabadwa Vitumbiko Chisoni, watulutsa mitengo yomwe amatchaja akayitanidwa kukayimba m’malo osiyanasiyana.

Mwachitsanzo, oyimbayu wati kuti akaimbe pa msonkhano wa ndale, amatchaja K3 miliyoni, misonkhano ya boma ndi ma bungwe K1.2 miliyoni pamene zochitika zina wati amatchaja K800,000 koma wati kukaimba ku mapemphero samatchaja kalikose.

Izi zatutumutsa Banda yemwe omutsatira amamutchula kuti Soja (Soldier) yemwe walemba patsamba lake la fesibuku kuti kuyika mitengo pa mbalambanda ngati momwe wapangira Pop Young nzachilendo kwa iye komaso zosayenera.

“Pa nkhani ya “Pop young” ine sindinatsutsane ndi mitengo kapena kunyazitsa mitengo Imene yaikidwayo, Sindine sponsor kapena manager wake sindingalamulire career yake.

“Chimene chili cha chilendo kwa ine, ndipo pa mbali ya Music management kulibeko, Ndicholemba mitengo ya mitundu ya Show mkuika pa mbalambanda ngati kuti akugulitsa mbale za chakudya mu Restaurant or kaunjika,” watelo Banda.

Iwo munkutsutsa kwawo ati, mitengo yokayimbira ku malo osiyanasiyana imatengera mgwirizano wa zinthu zingapo monga; nthawi ya zochitikazo, malo azochitikazo komaso mtundu wa zochitikazo.

Banda wati munthu akayankha zonsezi mpamene mitengo imapangidwa ndipo anenetsa kuti sizolondora kuyikiratu mitengo ngati momwe wapangira oyimba mzakeyu.

“Ndikupatseni Chitsanzo Mukuti political Rally ndi K3million okay fine. Mukundiuza kuti kachipani kakang’ono mungakapatse mtengo chimozi-mozi ndi Chipani chachikulu? (example) Chikomeni Vs MCP. Ma crowds awo ndiosiyana wina afuna zida zambiri wina zochepa mutchaja chimodxi modzi?

“Mukuti Corporate price 1.2 million well no problem. koma akati corporate Amanena ma company kodi ndiye kuti company yaikulu for example Ngati sunbird mungaipatse ntengo umozi ndi the grand paris hotel?

“Olo titayerekeza ma chalichi khwimbi la anthu lomwe mukalipeze ku for example ku ECG ndi kwa Habakuku, kkkkkk zingafanane?” wadabwa Banda.

Banda walangiza oyimba mdziko muno kuti asamapusitsike akaona mitengo pa intaneti ya oyimba akuluakulu pa dziko lonse ponena sizikhala zowona, wati ambiri amayika mitengoyo kufuna kuzikweza chabe.

Nkhaniyi yawutsa mpungwepungwe pa fesibuku kaamba koti ena akugwirizana ndi zomwe wayankhula Banda pamene ena akuti sakuona vuto lili lonse pa zomwe wachita Pop Young poyika mitengo take poyera.

Advertisement