Mthengo mudalaka njoka: De Jongh akulingalira zobanduka

Advertisement
Wanderers faced Silver Strikers at Kamuzu Stadium

Mphunzitsi wa mkulu wa timu ya Silver Strikers, Hendrikus Pieter de Jong yemwe ndiochokera m’dziko la Netherlands wati akuona kuti mpira wa ku Malawi wamulaka ndipo wati akuganiza kuti apite dziko lina.

De Jongh wayankhula izi dzulo pakutha pa masewero omwe timu yake ya Silver Strikers yagonja ndi chigoli chimodzi kwa chilowere ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa masewero omwe anachitikira pa bwalo la masewero la Kamuzu mumzinda wa Blantyre.

Mphunzitsiyu akuloza chala yemwe anaimbira masewerowa, Mayamiko Kanjere ponena kuti mayimbilidwe ake pa masewero alero asonyezeratu kuti anthu ambiri ali naye zifukwa.

Oyimbirayu anapereka khadi lofiyira (red card) kwa De Jongh mchigawo chachiwiri kaamba kosasunga mwambo pomwe timu yake imatsalira mchigawo cha chiwiri cha masewerowa.

Iye wati akuona kuti ndi kwabwino kuti atule pansi udindo wake ku timu ya Silver Strikers ndipo akapitilize kuphunzitsa mpira ku matimu a mayiko ena.

“Izizi zalowa zifukwa. sitediyamu yonse inaona kuti palibe chomwe ndinapanga cholakwika. Mwina ndi nthawi yoti ndi tsanzike kwa aliyese ndi kupita ku kaphunzitsa ku mayiko ena,” watelo De Jongh.

Miyezi yapitayo, De Jong anapatsidwaso chiphaso chofiyira kaamba kosasungaso mwambo ndipo wakhalaso akudzudzula atsogoleri ampira wa miyendo m’dzikomuno kuti asinthe kayendetsedwe ponena kuti zambiri zikulakwika.

Pamasewero omwewa, wachiwiri kwa De Jongh, Peter Mgangira, mmphunzitsi wa otchinjiliza pa golo, Sibusiso Padambo, komanso m’modzi mwa anyamata otseka kumbuyo Nickson Nyasulu, anapatsidwaso khadi lofiyira.

Advertisement