Gule kwawo: dela la mfumu yayikulu Chimutu ku Lilongwe, laletsa vilombovi kumapemphetsa m’misewu komaso kupezeka m’masukulu ndi m’misika, ndipo ati zikapezeka zikuchita izi zidzigwidwa ndi kukasiyidwa ku polisi.
Izi zili mu chikalata chomwe dela la mfumu yayikulu Chimutu latulutsa chodziwitsa anthu komaso akuluakulu a madambwe za malamulo atsopanowa ndipo chikalatachi chasayinidwa ndi mafumu asanu (5), a pansi pa mfumu yaikulu Chimutu.
Mwa zina, malamulo atsopanowa aletsa gule wa mkulu kutuluka chisawawa ponena kuti akuyenera kumatuluka pamiyambo yoyikika yokha yokha monga maliro, ziliza, zizangala ndi miyambo ina.
Mafumuwa ati gule wamkulu aliyense azitilukira kudambwe ndipo azidziwika dambwe lomwe akuchokera ndipo azikabwerera kudambweko ukatha mwambo omwe anatulukira.
Kuwonjezera apo, mafumuwa alamura kuti gule wamkulu wamtundu wa Kamano, Kanyamzizi asapezekenso mudera lonse la gogo chalo Chimutu ndipo aletsaso gule wa mtundu uliwonse kunyamula zikwanje.
“Gule wamkulu asapezeke pa sukulu, pa chipatala, tchalitchi ndi malo ena onse aboma ndiponso mmalo omwela mowa ngati m’ma bala. Gule wamkulu asapezeke akuyendayenda m’misewu kumavutitsa anthu kaya kupephetsa ndalama kuphatikizapo malo ena onse.
“Gule wamkulu azipeze pamiyambo ya Maliro, Ziliza, Zizangala ndi miyambo ina yovomerezeka ndipo mwambo ukatha zibwerere kudambwe. Ana a sukulu azimeta pa msinkhu osachepera zaka 18 ndipo azipezeka kuguleko nthawi ya holide,” atelo malamulo atsopanowa.
Azimayi awuzidwa kuti asamete ku gule wamkulu popanda zifukwa zomveka bwino ndipo akaumilira kumeta azilipira K50,000 komaso aliyese woyeserera kaliridwe, kaimbidwe ka gule wamkulu, azizengedwa mlandu osambula gule wa mkulu ndipo adzilipitsidwa.
Mafumuwa alamulaso kuti gule wamkulu aliyese akapezeka akuphwanya malamulo atsopanowa, achitetezo, mafumu ndi amaudindo akudelari ayenera amugwire ndi kukamupereka ku polisi iliyose.
“Gule wamkulu aliyense ovutitsa anthu m’misewu kumapephetsa ndalama m’misika ndi malo alionse a bizinezi ndi kumachitanso mchitidwe uliwonse wosavomerezeka, ameneyo sigule weniweni koma woyeserera gule wamkulu, chotero achitetezo, Mafumu ndi amaudindo onse amugwire ndi kukamupereka ku Police, ndi wambanda ameneyo,” watelo mbali ina ya malamulowa.
Malamulo wa awuza akuluakulu amadambwe kuti miyambo iliyonse yokhudzana ndi gule wamkulu monga maliro, ziliza, zizangala/mipalo, azipititsa uthenga kwa mfumu yayikulu Chimutu ndipo aliyense ophwanya malamulo akuderawa aziyimbidwa mlandu ndikulipitsidwa.
Ena mwa mafumu omwe asayinira malamulo aysopanowa ndimonga; GVH Mthyoka, GVH Kafulatira, GVH Simiyoni, GVH Chauwa komaso VH Msambira 1.