Kwavuta ndipo kuli moto buu ku tsamba la nchezo la thwita kaamba koti mwini wake Elon Musk akuti akufuna mfiti zoti azilembe ntchito.
Nkhaniyi inayamba pomwe katswiri ochita zisudzo otchedwa Megan Fox wa m’dziko la America anayika pa tsamba lake la thwita zithuzi za ana ake amuna atavala zovala zachikazi.
Izi zinakwiyitsa anthu ochuluka omwe anati Fox akuwaphuzitsa ana akewa omweso anawamanga tsitsi litalilitali, khalidwe loyipa.
Oyankhula pa zinthu zosiyanasiyana otchedwa Robby Starbuck anabwera poyera ndikulemba pa tsamba lake la thwita kumuuza Fox kuti asiyiletu kuchitira ana akewo nkhaza za mtundu ngati umenewu.
Koma Fox sanachilandire bwino chidzudzulocho ndipo mmalo mwake anayamba kumusambwadza Starbuck kwinaku akumuuza kuti adzijama yake.
Fox anapitilira kumuopseza Starbuck kuti waputa mavuto nkhomola ndipo ochita zisudzoyu anamuopseza Fox kuti akamutambila ku nyumba kwake.
“Tsopano Megan Fox akuwopseza kuti azichita mwambo wodya nyama ya mtembo kunyumba kwanga. Ichi chingakhale chisankho cholimba mtima/chopusa mu TN. Ngati cholinga chake chinali kuwoneka wopenga, mishoni yakwaniritsidwa! Tsopano anthu akudziwa kuti nayenso amachita ufiti,” anatelo Starbuck.
Potsatira zomwe zachitikazi, mwini wake wa thwita a Musk nawo anachita nthabwala kudzera pa tsamba lawo thwita.
Munthabwala yawoyi, a Musk anati iwo akufuna mfiti komaso anthu ena okopa anthu kuti awalembe ntchito ku kampani ya thwita.
“Ndikufuna kulemba ntchito wachiwiri kwa mtsogoleri wa afiti (VP of witchcraft) komaso wokopa,” adatero Musk patsamba lake la thwita.
Nthabwala ya Musk yatekesa tsamba la nchezoli pomwe anthu ochuluka akupitilibe kuikira ndemanga pa nkhani ya kusemphana chichewa kwa Fox ndi Starbuck.
Pofika lachiwiri madzulo, anthu pafupifupi 45 miliyoni anali atawona zomwe analemba Musk, ndipo nthabwalayi inalandira ndemanga zoposa 7000.
Musk adayamba kutsogolera kampani ya thwita mchaka cha 2022 atayigula pa ndalama zokwana 44 biliyoni za m’dzikola America.
Follow us on Twitter: