Chuluke chuluke ndi wa njuchi koma umanena yomwe yakuluma, a Malawi ochuluka awonetsa kugwa mchikondi ndi nyimbo yomwe yatenga kale malo ’Pano’ ya Shaffie Phiri yemwe amadziwikaso kuti Driemo.
Munyimboyi yomwe ndiyachikondi ndipo yatulutsidwa la chitatu sabata ino, munthu osweka mtima akudandaula kaamba ka kutha kwa ubwezi ndi okondedwa wake.
Odandaulayo akufusa bwezi lake lomwe lamusiyalo kuti mchifukwa chiyani wamusiya pomwe anamuyambitsa kuchita zinthu zosakhala bwino monga kumwa mowa komaso kusuta fodya wammphuno, ndipo osiyidwayo modandaula akumufusa wachikondi wakaleyo kuti ‘kodi ndaipa pano?’
“Kodi ndaipa pano?Ndakubhowa pano?Zosezija unandiphunzitsa Zikaipe pano?
“Unandiyambitsa shisha, mowa mesa ndiiwe? Iwe naine ku makalabu everyday (tsiku lili lonse) Lero mukuti Khalidwe la banja mwaine mulibe. Kodi ndigemu yamtundu wanji you are playing (ukusewera). Nde umkandisinthiranji?Umkandisinthiranji?Umkandisinthiranni bebe”
Nyimbo ya ‘Pano’ yomwe kanema wake wajambulidwa ndi mmodzi mwa anamanyonyolo pazojambula nyimbo, Twice P, ikumapeleka chidwi ukamayiwonera kaamba koti oyimba ochokera m’boma la Ntchisiyu wagwiritsa ntchito zinthu zamakono, mavalidwe opatsa chikoka komaso dona lomwe ambiri akuti ndi chiphadzuwa.
Podziwa kuti kutsutsa galu mkukumba, mmene pamatha maola makumi awiri ndi mphambu zinayi (24) chitulukireni nyimboyi, anthu opitilira chikwi zana limodzi (100,000) anali ataionera nyimboyi pa yuchubu (YouTube) zomwe sizimachitikachitika.
Kuonjezera apo, ena mwa anthu omwe anathilira ndemanga za nyimboyi patsamba la fesibuku la Driemo omwe ndikuphatikizapo oyimba monga; Piksy, Phyzix, Kell Kay, Rashley, Jay Jay Cee, kungotchulapo ochepa chabe, avulira chisoti oyimbayu ponena kuti nyimboyi ndi mtunda wina.
Komabe poti mvula ikagwa kuchuluka zoliralira, ena adzudzula oyimbayu kaamba kopota tsitsi ngati mzimayi pomwe enaso ati nyimbo ya ‘Pano’ siyabwino kwenikweni koma akuti yatchuka kaamba koti Driemo amakondedwa ndi azimayi.
“Nyimboyo si bomba ai, komano kungoti azimai amamukonda kwambiri ndiye olo ataimba zofoila, kwa iwowo amaonabe kuti ndi yabwino kozi mmaganizo mwao anakhazikisa kuti iyeyo ndi oyimba wabwino,” anatelo munthu wina poikira ndemanga za nyimboyi patsamba la fesibuku la Malawi24.
Iyi ndikanema yachitatu ya oyimbayu yemwe chaka chatha walandira mphoto ngati oyimba wachimuna yemwe anaimba bwino mchakacho ndipo nyimbo zake zina zodziwika kwambiri ndi monga ‘Compensation’ komaso ‘Mojo’.
Follow us on Twitter: