Nthawi ya DPP katangale analipo koma sanafike apapa — Ben Phiri

Advertisement

Phungu wadera lapakati m’boma la Thyolo a Ben Phiri, adzudzula boma la Tonse kaamba kosaonetsa chidwi pofuna kuthetsa katangale mdziko muno ndipo ati mu ulamuliro wa DPP katangale analipo koma ati sanafike mlingo omwe wafika pano.

A Phiri omwe amayankhula izi kwa atolankhani lachinayi mumzinda wa Lilongwe pakutha pazokambirana za nyumba ya malamulo zomwe zili nkati, anati chibadwire chawo sanaonepo ulamuliro wa katangale kuposa wa Tonse.

Iwo anauza atolankhani kuti chokhumudwitsa chachikulu nchakuti zipani zomwe zili mumgwirizano wa Tonse pano, nthawi yomwe zinali mbali yotsutsa boma, zinkaloza chala chipani cha DPP chomwe chinali cholamulira, kuti chikulimbikitsa katangale.

A Phiri omwe anapepesa pa katangale yemwe analipo nthawi ya DPP, ati ndizovetsa chisoni kuti nkhani za katangale zafika posauzana mdziko ngakhale kuti akuluakulu a mgwirizano wa Tonse ankalonjeza nthawi yokopa anthu kuti iyi idzakhala mbiri ya make dzana akadzalowa m’boma.

“Pomwe sindili okhutitsidwa ndipo ndipitilira kumenya nkhondo, ndi nkhani ya katangale. Muthakukumbukira kuti munali mnyumba ya malamulo yomwe ino momwe ankatidzudzura pankhani ya katangale pomwe iwo anali mbali yotsutsa boma.

“Zoonadi katangale analipo nthawi yathu ndipo tinapepesa komaso ine pandekha ndinapepesa kwa a Malawi, tikanatha kuchita bwino, koma fuso mkumati; pali kusintha tsopano? Pano katangale wafika poipitsitsa. Ili ndi boma loipitsitsa lomwe ndaliona chiyambireni,” watelo Phiri.

Apa phunguyu wauza akuluakulu a mgwirizano wa Tonse kuti ayambe kuchita zinthu zomwe analonjeza a Malawi nthawi yokopa anthu ndipo ati izizithandiza kuti dziko lino lisinthike komaso lipite patsogolo pankhani za chitukuko.

Chatsitsa dzaye kuti a Phiri ayankhule zonsezi ndi nkhani yokhudza kusakazidwa kwa ndalama zankhaninkhani za mundondomeko yazipangizo zaulimi zotsika mtengo.

Iwo ati ndizodabwitsa kuti boma kudzera ku
Smallholder Farmers Fertilizer Revolving Fund of Malawi (SFFRFM) inalowa mumgwirizano wa ndalama zoposera K170 billion ndi kampani ina yaku UK, Auzano Capital Management.

Apa a Phiri ati akuganizira kuti akuluakulu ena aboma akukhudzidwa ndi nkhaniyi ponena kuti ndizosamvetsetseka kuti boma likalowe mumgwirizano wa ndalama zochuluka chonchi ndi kampani yomwe akuti siinathe chaka chiikhazikitsileni.

“Vuto langa ndi mmene boma likuyendetsera chuma cha a Malawi. Sindikumavetsetsa mpaka pano kuti kampani yomwe siinathe chaka chiitsegulireni ikavomelezedwe kupanga mgwirizano ndi boma pa ndalama zoposera $170 million. Pali wina wake kumbaliku akukhudzidwa, ndipo ndithakuyankhula mopanda mantha, titati tifufuze bwino bwino tikapeza kuti pali wina wake,” anaonjezera a Phiri.

Advertisement