Osamatengeka ngati mwana wa zaka ziwiri akaona chimsope — Chilima auza a Gotani Hara

Advertisement
Catherine Gotani Hara

Wachiwili kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima wasambwaza sipika wa nyumba ya malamulo a Gotani Hara ati kamba kosokoneza mgwilizano wa pakati pa Kongeresi ndi UTM.

Polankhula lachisanu pamene amalankhula kwa owatsatila komanso a Malawi malinga pamene anatchulidwa kuti ndi katswiri wa katangale, a Chilima anati anthu ena mu mgwilizano wa Tonse akomedwa ndi udindo.

“Mgwilizano uwu usaonongedwe chifukwa choti anthu ena alawa udindo ndipo aumva kukoma,” anatelo a Chilima. Iwo anaonjezelapo kuti anthu ena akunga mwana wa zaka ziwili oti waona yogeta mu shopu.

Chilima

Kunena kwa a Chilima, anthu ena akuyesa kuti iwo amazembelela sipika wa nyumba ya malamulo Mayi Gotani Hara amene analankhula pa mgonelo wa chipani cha MCP kuti zivute zitani a Chakwera aimilanso 2025. A Hara anati Mulungu ndiye anaikapo a Chakwera pa mpando.

A Chilima anati malinga ndi mgwilizano umene ulipo, a Chakwera akuyenela asiye boma 2025 kuti a Chilima atengepo.

Follow us on Twitter:

Advertisement

3 Comments

  1. Komatu penapake achiloma akuphatikiza nkhani,tipange Kaye za Sanett Zata

  2. Malawi wathu asakhale ngati ndiwa munthu modzi amene akuziwona kuti akhoza kumasintha malamulo oyendetsera dziko kuchokera kuchipani china kupitanso chipani china. Kuyambira kale Malawi ndi dziko lathu lowopa mulungu ndipo malamulo athu oyendetsera dziko amakhazikitsidwa ndi anthu owopa mulungu osati munthu wina kungotenga malamulo ake ndicholinga chofuna kupanga ma business ake mudzina loyendetsera dziko

Comments are closed.