Bwato satsitsilana pakati pa nyanja — Usi

Advertisement

Wachiwiri kwa pulezidenti wa chipani cha UTM a Michael Usi omwenso ndi nduna ya zokopa alendo achenjeza zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM kuti wina asatsitse nzake mu bwato pakati pa nyanja.

A Usi amayankhula izi dzulo pa mwambo okumbukila mtsogoleri woyamba wa dziko lino a Kamuzu Banda.

Ku mwambowu kunalinso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera yemwe analowa mu boma mu 2020 pomwe chipani chawo cha MCP chinapanga mgwirizano ndi chipani cha UTM chomwe mtsogoleri wake ndi Saulos Chilima, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

A Usi anati UTM ndi MCP anayamba ulendo nthawi imodzi ndipo sibwino kuti wina pano ayambe kuwuza nzake kuti atsike.

“Tinakwera bwato pa gombe limodzi. Wina asayambe kuti awa bwanji atsike,” anatero a Usi.

A Usi anatinso anthu a MCP ndi UTM ndi amodzi ndipo anachenjeza onse omwe akuchita chibwana mu zipanizi kuti asiye.

Iwo anaonjezera kunena kuti Mulungu anapereka dziko la Malawi ndi anthu ambiri a nzeru ndipo palibe chifukwa choti anthu adzivutika ndikumayimba nyimbo kuti vinyo watha.

Malingana ndi a Usi, vinyo alipo koma chofunika ndi choti boma litenge vinyo likawapatse anthu.

Poyankhulapo za kagwilidwe ntchito ka m’boma, a Usi anauza a Chakwera kuti achotse ntchito ogwira ntchito m’boma omwe akumachedwetsa zinthu.

“Ndikukamba izi pokufunilani zabwino, ena amabwera kumakusekelelani ngati akudziwa ntchito, ata sadziwa,” anatero a Usi.

Mawu omwe a Usi ayankhula adza pomwe pali mphekesera yokuti pali kusagwirizana pakati pa a Chakwera ndi a Chilima maka pa nkhani ya yemwe adzakhale woyimira mgwirizano wa Tonse mu chaka cha 2025.