
Ubale omwe unayamba zaka zitatu zapitazo pakati pa timu ya Mighty Wanderers ndi kampani ya Mukuru wathapo tsopano.
Mu kalata yomwe Wanderers yatulutsa yomwe watsimikiza ndi mlembi wa board ya timuyi, a Chancy Gondwe komanso wamkuru owona za malonda ku kampani ya Mukuru, a Brandon Mncube ati, ubalewu wazilalapo awiriwa atagwirizana kusayenderanso limodzi.
“Mbali ziwirizi zikulengeza kuti zagwirizana kuti zisapitilizane mgwirizano wa thandizo pakati pa Mighty Wanderers ndi Mukuru,” yalembedwa choncho kalata mchizungu.
Timu ya Wanderers idatsimikikizirana mgwirizano wa ndalama zokwana 175 million kuti Wanderers iyambe kutchedwa Mighty Mukuru Wanderers ndipo timuyi yayamika kampani ya Mukuru chifukwa cha ubale omwe unalipo.
Sabata latha, Wanderers yatsimikizirana mgwirizano wa ndalama zokwana 100 million pa chaka ndi kampani ya mlosera ya 888 bets.
Mighty always move forward. Let’s move forward despite mukuru