Ngakhale boma limamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti m’dziko muno mulibe ufiti, mkulu wina m’boma la Zomba wabwera poyera kutsimikiza kuti ufiti ulipo padziko lapansi pano ndipo wati iyeyo ndi wankulu wa afiti.
Mkuluyu yemwe dzina lake ndi John Awufi wa m’mudzi mwa Mbuka dera la mfumu yaikulu Kumtumanji ku Zomba, amayankhula izi mu pologalamu ya ‘Tamvani’ yomwe inaulutsidwa Lamulungu pa wailesi ya Times.
Bambo Awufi omweso akuti amadziwika ndi dzina loti Chimera anati amakhala odabwa kuti mpaka pano boma kudzera m’malamulo a dziko lino limati ufiti kulibe pomwe iwo akuti ndi namandwa ya afiti onse.
Iwo anati koyamba anazindikira kuti kunja kuno kuli ufiti mu mchaka cha 2008 pamene afiti ena anawameta tsitsi lawo lammutu mmatsenga usiku atagona koma ati panthawiyi iwo anali asanaphunzile ufiti komaso kuwuluka.
A Chimera anati zitachitika izi anakapeza mkulu wina dzina lake Sam yemwe akuti amadziwa mankhwala a zitsamba ndipo atamufotokozera za mazangazimewo, anampatsa mankhwala ndipo usiku wa tsiku lomwelo tsitsi linabwelera mmutu mwake.
Iwo anati kuti aphunzile ufiti ndikuuluka, anachita kumwa chithumwa chomwe mkati mwake munali timitengo tiwiri tomwe akuti timamupangitsa munthu amene ndi mfiti kuchita zosiyana ndi zomwe munthu wabwinobwino amachita.
“Paufiti sitimavala malaya, zovala zonse timavula. Powuluka nkhope imasintha, siimafanana ndimmene amaonekera munthu. Pamakhala mitengo iwiri nde amaisoka mkukhala kachithumwa komwe amakupatsa kuti umwe usanaphunzire ufiti nde ukamwa imalowelera mthupi ndipo ndiyomwe imakupangitsa kuti uzikwanitsa kusanduka,” anatelo a Awufi.
Iwo anati munthu yemwe akufuna kupita kokatamba, kukada amayamba ndikudziongola ndipo mkati mwakudziongola ziwalo monga milomo, manja, maso komaso miyendo zimayamba kusololoka ndipo kenaka amadumpha m’phika wamankhwala ndikutulukira pangodya yanyumba.
Apa mkuluyu anati afiti ambiri amagwiritsa ntchito lichelo ngati ndege yawo momwe akuti amatha kukwelamo anthu osaposera 15 ndipo watiso ena amathaso kukwera tsache, chipande ndi mthiko koma wati izi pamakwerapo anthu ochepelako.
“Pamakhala m’phika ndipo mumaponyedwamo mphinjiri, nde timadumpha m’phika umenewo ndipo omwewo umakhala ulendo okatamba ndipo kuuluka kwakwe timakwera lichelo lomwe mumatha kukwana anthu pakati pa 10 ndi 15. Izi sikuti ndikungokamba, ndakhala ndikuzichita,” anaonjezera choncho Awufi.
Ngakhale akukamba zonsezi, mkuluyu akuti pano samatambanso kaamba koti munthu wina yemwe sanamutchule anamupatsa mankhwala omwe anapangitsa kuti asanze chithumwa chomwe anameza pomwe ankaphunzira ufiti.
A Chimera ati pano amachita nsanje akamuona munthu akutamba ndipo ati pano nawo analowa ntchito yochotsa anzawo ufiti.
“Ndinakumana ndi munthu wina amene anandisanzitsa zithumwa zonse zomwe zinali mmimba mwanga ndipo ndinapeza mpumulo chifukwa poyambapo ndisanasiye kuwuluka ndinkangogona ndi masana omwe paliponse.
“Nditasiya ufiti ndinakhala masitala (master) wa afiti moti pano ndimachotsaso amzanga ufiti chifukwa ndimapanga nsanje kuti ine ndimalephera kuuluka nde nawoso asamauluke. Ndikunenetsa kuti ufiti ulipo ndithu, ine ndi mboni,” anaonjezera choncho a Chimera.
Koma ngakhale a Chimera akuti anasiya kuwuluka, ati pano amapangabe zamatsenga monga chingwe kuchisandutsa njoka ndipo ati amaituma kupita komwe iwo akufuna komaso ati amakwanitsa kuika chinthu m’botolo ngakhale chikule bwanji.
Nkhaniyi ikubwera pomwe mwezi wathawu bungwe lowona za malamulo la Malawi Law Society (MLS) latulutsa zotsatira zakafukufuku yemwe linapanga m’mbuyomu pankhani ya ufiti ndipo lapeza kuti ufiti ulipodi mdziko muno.
Apa bungwe la MLS lati ndikofunika kuti lamulo lomwe limati ufiti kulibe liunikidweso ndi adindo ndipo onse amene azipezeka olakwa pankhani yaufiti azilandira chilango.