Apolisi amanga m’neneri kamba komuganizira kuti anagwililira

Advertisement

Apolisi ku Ntcheu amanga a Joseph Gamaliyele a zaka makumi awiri ndi mphambu zisanu, 29, powaganizira kuti agwililira mtsikana wazaka makumi awiri ndi mphambu zitatu.

Malingana ndi m’neneri wa a Polisi ku Ntcheu a Rabbeca Kwisongole ati mzimayiyu ndi nkhosa ya mu utumiki wa Ebenezer Niss .

“Lolemba pa December 20, 2021 mayiyu anapita ku phiri kuti akapemphere, ali konko analandira foni kuchokera kwa M’neneri kufusa komwe iye anali. iye atanena kuti ali ku phiri M’neneri anamulondola komweko ndipo anayamba kumunyengelera kuti agone naye. Atakana, iwo anamugwira ndikugonana naye momukakamiza” anatero a Kwisongole.

A Gamaliyele akuyembekezera kukawonekera ku khoti posachedwapa kukayankha mlandu ogwililira.

Iwo amachokera ku Dedza mfumu yayikulu Tambala.

 

 

 

Advertisement