Mayi wa zaka 26, Lusayo Kaliza, ali m’manja mwa a polisi ku Lilongwe kamba koganidzilidwa kuti anaba mankhwala ndi zipangizo zina zogwiritsila ntchito pa chipatala cha Bwaila.
Iwo amachokera m’mudzi mwa Mchochoma mfumu yayikulu Kamenyagwaza ku Dedza.
Malingana ndi m’neneri wa a polisi ku Lilongwe Sub Inspector Hastings Chigalu, mayiyu amagwira ntchito pa chipatala cha Bwaila kumbali ya ana osapyola dzaka zisanu .
“Iye anavomera kuti anatengadi mankhwala ndi zipangizo zina pamalo a ntchito, iye anagwidwa ndi alonda atayimisa galimoto lake la Dahatsu Mira pazipata zotulukira kuchipatala ndipo anakamupeleka ku polisi ya Lilongwe”
Zina mwa zinthu zomwe anapezamo ndi mulingo pafupi fupi 30 LA, 50 vials wa X -Pen, malita 10 a RIL, ma bokosi 11 amagulovu, mabotolo awiri a Amoxicillin, mabotolo awiri a Myconova , mabotolo awiri a Paracetamol, mabotolo awiri a Paracetamol Syrup komanso paketi limodzi la zotchinjira ku khope.
Izi zikudza patangodutsa masiku ochepa chabe a polisi atamanga ogwira ntchito za umoyo pachipatala cha Kamuzu kamba kakuba ma gulovesi.
A Chigalu anapitilira kunena kuti kafukufuku pankhaniyi akupitilira ndipo mayi akuyembekedzera kukawonekera mu khoti posachedwapa kuti akayankhe milandu wakuba pamalo a ntchito zomwe ndidzusutsana ndi malamulo aakulu adziko lino gawo 283.