Akuluakulu aku nyumba ya boma ati sakuona vuto lililonse pakusankhidwa kwa mwana wa mtsogoleri wa dziko lino Violet Chakwera Mwasinga kukhala mlembi ku office ya oyimilira dziko lino ku Brussels.
Izi ndimalingana ndi oyankhulira mtsogoleri wa dziko lino a Brian Banda omwe anena izi Lolemba m’mawa pansonkhano wa olemba nkhani omwe umachitikira ku nyumba ya boma ya Kamuzu mumzinda wa Lilongwe.
A Banda anati ndizokhumudwitsa kuti anthu ambiri akuloza chala mtsogoleri wa dziko lino pakusankha mwana wawo wankazi, Violet kukakhala mlembi wachitatu ku ofesi ya kazembe wa dziko lino ku Brussels.
Iwo anati mtsogoleri wa dziko lino wasankha anthu mmaudindo a boma ochuluka ndipo ati ndizodabwitsa kuti anthu akulankhula zambiri pakusankhidwa kwa Violet yemwe ati tchimo lake ndiloti ndi mwana wa mtsogoleri wa dziko, zomwe ati ndizolakwika kwambiri.
Oyankhulira mtsogoleri wa dziko linoyu anati Violet ali ndi zonse zomuyenereza kukhala pa udindowu komaso ati mwana wa mtsogoleri wadzikoyu anadusa mundondomeko zonse zomwe zimatsatidwa pomwe munthu akusankhidwa pa udindo wa boma.
“Mtsogoleri wadziko lino wasankha anthu mmaundido aboma oposa 2000 koma ndizodabwitsa kuti mukuona vuto pakusankhidwa kwa munthu mmodzi amene wadutsa mundondomeko yonse yosankhira anthu mmaudindo aboma komaso ali ndi mapepala oyenelera ndipo tchimo lake lake ndilokhala mwana wa mtsogoleri wa dziko.
“Choncho ife ku nyumba yaboma tikuona kuti palibe vuto lililonse. Anthu onse omwe akusankhidwa ndi mtsogoleri wadziko lino, ndiwoyenera ndipo adutsa ndondomeko zonse. Zoona mukufuna asapite chifukwa ndimwana wa mtsogoleri wadziko? Sibwino choncho,” watelo Banda.
A Banda anaonjezera kuti nyumba yaboma inakavetsetsa za madandaulo omwe anthu akupeleka pakusankhidwa kwa Violet pokhapokha osankhidwayu anakakhala kuti alibe zomuyenereza komaso sanadutse mundondomeko yosankhira anthu mmaudindo aboma.
Pakadali pano anthu mmasamba amchezo akugawana kanema wa zomwe anayankhula a Chakwera pomwe anali mkulu wa zipani zotsutsa ndipo ankadzudzula a Peter Mutharika pakukula kwa mchitidwe oyika achibale m’maudindo a boma.