M’modzi mwa anthu olankhulapo pa momwe zinthu zikuyendela mdziko lino a Idriss Ali Nasah wati asumila nthambi ya boma yowona ngozi zogwa mwadzidzidzi ngati silipeleka lipoti lofotokoza bwinobwino momwe ndalama za boma zokwana K6.2 biliyoni zagwilitsidwira pothana ndi mliri wa Covid-19.
Pa 17 Januwale pulezident wa dziko lino a Lazarus Chakwera mu uthenga wawo opita kwa a Malawi, anazizimutsa anthu ponena kuti boma la mugwilizano wa Tonse lawononga ndalama pafupifupi K6.2 biliyoni ku nthambi yapadera yolimbana ndi mliriwu.
Iwo mkufotokoza kwawo adati K60 miliyoni yagwira ntchito popangila mikumano, K535 miliyoni pobweletsa a Malawi omwe anavutika ku Joweni, K185 miliyoni pofalitsira uthenga, K580 miliyoni polondera malire a dziko, K72 miliyoni pothandizila anthu omwe adachitilika nkhaza mu nthawiyi, K100 miliyoni kupopera masukulu ndi mankhwala, K50 miliyoni kuwonesetsa kuti mmalo ogwilamo ntchito ndi otetezedwa komanso K50 miliyoni kukoza malo apadera osungako odwala muliriwu.
Uthengawu anthu ambiri anazidzimuka nawo ponena kuti ndalama zikutchulidwadzi sizikugwilizana nkomwe ndi ntchito yomwe yagwilika.
Ambiri omwe anachokera ku Joweni adalankhulapo kuti boma silinapelekepo kanthu kena kalikose ndipo iwo amalipila okha tiketi ya basi komanso chipepala chowalola kuti atha kuyenda kubwelera kumudzi chotchedwa Covid19 certificate.
Pa 18 Januwale a Idriss Ali Nasah analembela kalata nthambi ya boma yowona ngozi zogwa mwadzidzidzi DODMA kuti amufotokozere bwino lomwe ndipo iye wati nthambiyi inamuwuza kuti ayipatse nthawi.
Ndipo lero Nassah walengeza kuti kufikira lolemba ngati samupatsa akasuma ku nthawi yowona za malamulo kuti akafotokodze bwino kumeneko.
Pothilila ndemanga, katswiri winanso olankhulapo momwe zinthu zikuyendela mdziko muno Joshua Chisa Mbele wati iye ngokonzeka kugwilana manja ndi a Nassah mpaka chilungamo chiwoneke poyera.