Kwabwera Mahule: Amayi ogulitsa chiwerewere akwiya

Advertisement

Amayi ogulitsa chiwerewere lero ku Lilongwe anachita zionetsero zosonyeza kukwiya ndi lamulo la boma lokuti malo omwera mowa azitsekulidwa 2 koloko masana ndikutsekedwa 8 koloko usiku.

Boma linaika malamulowa pofuna kuthana ndi mliri wa Corona omwe wavuta kwambiri makamaka mwezi uno.

Koma amayiwa akwiya ndi ganizoli ndipo lero anayenda kuchoka pa bwalo la Community kupita ku maofesi a khonsolo ya mzindawu. Amayiwa ananyamula mapepala olembapo mauthenga ndipo nyimbo yotchuka yoti Kwabwera Mahule imamveka pa masipikala.

Amayiwa akuti malo azachisangalalo ndi maofesi awo ndiye akumapanga ndalama zochepa pano chifukwa malowa sakutsekulidwa nthawi yaitali.

Malingana ndi amayiwa, iwo akufuna mashabini ndi ma bala azitsekulidwa 2 koloko mpaka pakati pa usiku kuyambira lolemba mpaka lachinayi.

Koma lachisanu mpaka lamulungu, amayiwa akufuna malowa azikhala otsekula m’mene amachitira mwa nthawi zonse popeza wikendi ndi pomwe makasitomala awo amapezeka ku malowa.

“Tikukhulupirira kuti madandaulo anthu amveka kubomako ndipo akonza monga ife tikufunira,” anatero a Zinenani Majawa omwe ndi otsogolera amayiwa.

Chikalata chawo amayiwa anakasiya ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe komwe m’modzi mwa akuluakulu a kumeneko a Hudson Kuphanga anayamikira a Mayi a malondawa pochita zionetsero zawo mwa bata.

Advertisement