Bweletsani katemela wa Covid, ndibayidwe ine – Mutharika

Advertisement

Kaya muziti ndi wa satanic, kaya mwina muzinamizana kuti cholinga chake ndi choti athene abambo, a Mutharika azipeleka kuti iwo ndi okonzeka kukabayidwa katemela wa Covid akangofika ku Malawi kuno.

Mtsogoleri opuma a Peter Mutharika wanena kuti iye ndi okonzeka kukalandila katemela wa Covid akafika, ndipo sazachedwa ndi komwe.

Polankhulana ndi mtolankhani wa Voice of America, a Mutharika ati iwo ndi okonzeka kuti abayidwe katemela ameneyu akapezeka. A Mutharika alankhula izi pamene pali mantha pakati pa a Malawi ena zokhudza katemelayu.

“Ine sindingakayike konse kukalandila katemelayu,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika amene ali ndi zaka 80 ali mu gulu la anthu oyenela kulandila katemela koyambilila akayamba kupezeka.

Pothililapo ndemanga pa mmene a Chakwera akutsogolelela a Malawi pofuna kuthana ndi mlili wa Covid, a Mutharika ati a Chakwera sakupanga zogwila mtima kwenikweni.

“Nkhani ngati zopeleka kangachepe kwa ovutika, a Chakwera sakupangapo kanthu pa zimenezi. Izo sizikundigwila mtima,” anatelo a Mutharika.

Iwonso anaonjezelapo kuti a Chakwera sanayeze a Malawi ochuluka zinthu zimene zikuika pa chiopsezo a Malawi ochuluka.

Advertisement