…anama kuti ndalama zaboma zinathandiza amalawi kuthawa Covid ku Joweni
A Malawi omwe anavotera mtsogoleri Lazarus Chakwera chaka chathachi awuzidwa ndi mtsogolerIyu kuti anachalira vimadzi vamphusi chifukwa iwo sali pano kukwaniritsa lonjezano lomwe ananena. Ena nkumati, m’busa Chakwera yemwe ndi mtsogoleriso wa dziko lino waiwala kale kuti lonjezo linadulitsa mutu wa Yohane.
A Chakwera mu nthawi ya kampeni analonjeza ntchito one miliyoni mu chaka choyamba, kutsitsa mtengo wa pasipoti, kuchotsa ndalama zomwe anthu amalipira polumikizitsa magetsi komanso madzi ndi kuonetsetsa kuti a Malawi akudya katatu.
Koma lamulungu a Chakwera anauza a Malawi kuti aiwale za malonjezowa chifukwa boma lawo lakumana ndi Namondwe ndipo chidwi cha boma lawo chili polimbana ndi mliri wa Corona.
Izi zakwiyitsa a Malawi ena omwe adzudzula a Chakwera kuti ankawanamiza pa nthawi ya kampeni. Dzulo, bungwe lomenyera ufulu la CDEDI linauza a Chakwera kuti atule pansi udindo kamba kopereka malonjezo omwe sangathe kukwaniritsa.
Mu mawu awo lamulungu, a Chakwera anauzanso anthu kuti boma lawo lagwirita nthito K6.2 biliyoni ndipo K535 miliyoni inagwira ntchito pobweretsa a Malawi osachepera 19,000 kuchoka ku South Africa.
Iwo anati ndalamazi mwa zina zinagwira ntchito yolipira thiransipoti, chakudya komanso pogona.
M’modzi wa a Malawi omwe anabwera kuchoka South Africa chaka chatha a Yamikani Kachingwe ati zomwe amanena a Chakwera ndi bodza la nkunkhuniza chifukwa a Malawi ochoka ku South Africa amalipira okha ma bus komanso Chakudya.
A Kachingwe anaonjeza kunena kuti boma linangopereka malo ogona ku Malawi kuno koma malowa monga masukulu ophunzitsira a polisi ndi a boma kale ndipo boma silimalipira kalikonse.
“Ndiye boma la a Chakwera linagwiritsa bwanji ntchito ndalama zonsezi? Angonena kuti ndalamazi anapangira mikumano ku Nyanja ndipo anagawana ngati ma allowance,” anateroa a Kachingwe.