Iwalani za malonjezo a campaign, sitima yakumana ndi Namondwe – Chakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera Malawi President

Kodi mukudikila ntchito 1 miliyoni, kutsitsa mtengo kwa passport, ngongole za achinyamata ndi amayi kufika pa 15 billion, kapena kulumikiza madzi ndi magetsi ulere? Mukudikila madzi a mphutsi, sizitheka zimenezo.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera wauza anthu amene akudikila kuti boma lake likwanilitse malonjezo a kampeni kuti ndi oduka mutu.

A Chakwera analengeza dzulo kuti boma lawo lakumana ndi namondwe amene awakanikitse kukwanilitsa malonjezo amene anapanga pofuna kutenga boma.

Iwo ananena izi pamene analengeza zomwe boma lawo lichite pofuna kuthana ndi matenda a Covid-19 amene alusa ndi kuluma mano mu dziko lino.

Mu mawu awo, a Chakwera analengeza kuti ayika ndalama za nkhani nkhani kuthana ndi matenda wa. Ndipo anaonjezelapo kuti izi zikhudza malonjezo amene anapanga nthawi ya kampeni.

“Pali anthu ena amene akumanena kuti tipange zinthu, koma osanena uko kuchoke ndalama. Uku ndi kupanda nzeru,” anatelo a Chakwera.

Iwo anapitiliza ndi kunena kuti a malinyelo akakumana ndi namondwe pa nyanja amasintha njila ndipo boma lawo nalo lisintha njila pa malonjezo a kampeni amene linapanga.

Lingalilo ili ladabwitsa anthu amene akuti malonjezo amene a Chakwera anapanga anapangidwa kunja kudakali namondwe wa Covid-19 kale.

“Kodi a Chakwera adziwa liti za Covid-19? Mesa nthawi yonse ya kampeni ija anali akudziwa kale kuti kuli Covid?” adabwa chotelo a Malawi okana kunamizidwa.

Advertisement

One Comment

  1. Idzi nde mbuzi za atsogoleri.
    Sakudziwa kuti atha kulowera kutiko kokapempha thandidzo la mtundu wa a malawi.
    3yrs to goooooo

Comments are closed.