Boma lati liyamba kukakamiza anthu kuvala zozitchingila ku nkhope ngati njira yochepetsa kufala kwa covid.
Mlembi mu unduna wa maboma aang’ono a Charles Kalemba anenaizi ku Lilongwe dzulo ndipo ati boma liyamba kusatila ndondomeko zomwe zinatsindikidzidwa kale chaka chatha.
Matenda otchedwa Covid 19 akupitilila kufala mdziko muno zinthu zomwe zayika pamupanipani adindo.
Lachinayi anthu opezeka ndi Covid anakwana 274 ndipo chiwerengero cha anthu omwe agonekedwa mu zipatala chafika 73.
Mneneri wa ndende mdziko muno a Chimwemwe Shaba atsimikiza kuti akaidi makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu pa zana apezeka ndi matendawa ku ndende ya Zomba.
Iwo anati ndendeyi mothandidzidwa ndi a digital health anayesa anthu makumi awiri ndipo anthu khumi asanu ndi awiri anapezeka ndi mliriwu.
Ndende ya Zomba imasunga akayidi pafupi fupi zikwi ziwiri mazana anayi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anayi.
Chiyambireni matenda a Covid ku Malawi anthu opezeka ndi korona ndi okwana, 7, 611, omwalira ndi okwana 203 pomwe ochira ndi 5,791.